Nyimbo 150
Mkate Wochokera Kumwamba
1. Atate wakumwamba,
Simusintha nthaŵi zonse,
Tiimba zitamando
Kuyeretsa dzina lanu.
Monga Mbusa wokonda,
Munatsogolera
Anthu anu akale,
Munapatsa mana.
Munawapatsa madzi,
Ndi kuthetsa ludzu lawo.
Anadza ku Kanani,
Ali okhuta okondwa.
2. Mana munawadyetsa
Anaimira Mwana’nu,
Anachoka kumwamba
Kudzawombolatu anthu.
Iye ndiye mkatewo;
Wochoka kumwamba
Anapereka nsembe,
Kutipulumutsa.
M’chikhulupiro tidye
Mkate M’lungu watipatsa;
E, nthaŵi zonse tidye,
Kuti tikhale oyera.
3. Mbiri ya mkate uwu
Tisabisire anjala,
Pokhalatu ndi nthaŵi,
Tidyetse ‘tinkhosa’ tonse.
Thandizani enawo
Kupeza cho’nadi,
Kuti apulumuke,
Ndi kudalitsidwa.
Pa Mbuyo pa nkhondoyo
Yaikulu Armagedo,
Tidzaimba kosatha,
Zitamando za Mulungu.