Nyimbo 105
Tamandani Woyamba Kubadwa wa Yehova!
1. Titame Woyambayo
—Woloŵatu nyumba—
Chilengedwere iye,
Amamvera M’lungu.
Anapanga zinthuzo
Zammwamba ndi m’dziko,
Monga womlankhulira,
Anena za M’lungu.
2. Pokhala ngati M’lungu,
Sanayese konse
Kupikisana naye
Mulungu wakeyo.
Koma nadzichepetsa
Nakhalatu munthu
Kukwezatu Yehova
Ndi kupatsa moyo.
3. Kristu anakwezedwa
Natukulidwadi
Kuimira Mulungu
Kuyeretsa dzina.
Adzatitchinjiriza
Pa Armagedopo,
Kuwononga adani,
Nadzetsa mtendere.
4. Tamatu Woyambayo!
Nena za Ufumu.
Lalikadi ponsepo;
Kunyumba ndi nyumba.
Mosamalitsa ndithu
Thandizatu ena.
Kuti atamandetu
Woyamba kubadwa.