Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/99 tsamba 7
  • Kodi Mukusamuka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukusamuka?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mungatani Kuti Muzolowere Mukasamukira Mumpingo Wina?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Nyumba ya Ufumu Yanu Mumaiona Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Mpingo Uyenera Kulimbikitsidwa
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Mpingo Uyenera Kutamanda Yehova
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 10/99 tsamba 7

Kodi Mukusamuka?

Pamene yankho la funso limeneli lili inde, pamakhala zinthu zambiri zimene inu ndi ena muyenera kuzichita. Mwa kutsatira ndondomeko yofunika ili m’munsiyi, mudzakhazikika mofulumira mu mpingo wanu watsopano.

(1) Mukangodziŵa kumene mukusamukira, mlembi wa mpingo wanu angapeze adiresi ya Nyumba ya Ufumu ya mpingo wanu watsopano. Mukafika kumeneko, mwamsanga fufuzani holo ndi kudziŵa nthaŵi za misonkhano ya mpingo. Ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, funsani akulu akuuzeni mpingo wa gawo limene mukukhala. Musachedwe kuyamba kupezeka pamisonkhano ndi kudziŵana ndi akulu akumeneko.

(2) Mlembi wa mpingo umene munali ndi wa mpingo wanu watsopano adzagwirizana zosamutsa makadi a Cholembapo Ntchito za Wofalitsa cha Mpingo, lanu ndi a banja lanu. Kalata yokudziŵikitsani idzatumizidwanso kwa akulu akumpingo wanu watsopano. (Onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 1991.) Komiti Yautumiki ya Mpingo ya kumeneko iyenera kuuza wochititsa phunziro la buku woyenera za kufika kwanu kuti aonane nanu ndi kukusonyezani gulu lanu latsopano la phunziro la buku.—Aroma 15:7.

(3) Ofalitsa onse mumpingo wanu watsopano ali ndi ntchito yosangalatsa yoti agwire—yodziŵana nanu bwino ndi kukupangitsani kuona kuti akulandirani. (Yerekezani ndi 3 Yohane 8.) Ndithudi, zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kumapezeka pamisonkhano kuti mulimbikitsane ndi kumangirirana ndi abale ndi alongo.

(4) Musadikire mpaka zonse za kusamuka kwanu zitatha kuti muyambe kuloŵa mu utumiki wakumunda ndi mpingo wanu watsopanowo. Pamene mutsogoza zinthu za Ufumu, zinthu zina zidzayenda bwino ndipo mudzakhala womasuka kwambiri kumalo anu achilendowo. (Mat. 6:33) Pamene mwakhazikika kunyumba yanu yatsopanoyo, mosakayikira mudzafuna kuitana ena a mumpingo kudzakuchezerani ndi kudziŵana nawo bwino.—Aroma 12:13b.

Kusamuka ndi ntchito yaikulu. Komabe, pamene onse amene zikuwakhudza achita zofunikira, sipadzakhala kufooka mwauzimu. Onse adzachita chidwi ndi ubale wathu wachikondi chachikristu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena