Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/09 tsamba 6-7
  • Kodi Nyumba ya Ufumu Yanu Mumaiona Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nyumba ya Ufumu Yanu Mumaiona Bwanji?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Malo Olambirira Yehova
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Tiyeni Tizikonza Malo Athu Olambirirapo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Tizilemekeza Malo Athu Olambirira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Mumalemekeza Malo Anu Olambirira?
    Nsanja ya Olonda—1993
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 4/09 tsamba 6-7

Kodi Nyumba ya Ufumu Yanu Mumaiona Bwanji?

1 Mofanana ndi chitsime cha madzi m’dera losowa madzi, Nyumba ya Ufumu ndi malo amene anthu amatsitsimulidwa mwauzimu. Anthu osiyanasiyana amabwera ku Nyumba ya Ufumu kudzaphunzira za Yehova. Iwo amaiona kuti ndi nyumba imene cholinga chake n’kulambiriramo Mulungu wathu, Yehova, basi. Kodi umu ndi mmene inunso mumaionera Nyumba ya Ufumu? Kodi mumayembekezera mwachidwi misonkhano, kucheza ndi abale ndi alongo, komanso kukagwira nawo ntchito zina?

2 Mungasamalire Nawo Nyumba ya Ufumu: Nyumba ya Ufumu imafunika kuyeretsa ndi kukonza mowonongeka chifukwa imagwiritsidwa ntchito pafupipafupi. Kodi mumayamikira mwayi womwe muli nawo wothandiza kusamalira Nyumba ya Ufumu? Muyenera kukhala ndi ndandanda yosasinthasintha yosamalira Nyumba ya Ufumu, mogwirizana ndi mmene imagwiritsidwira ntchito. Aliyense ayenera kugwira nawo ntchitoyi, ngakhale ana. Tikamachita zimenezi, aliyense adzadziwa kuti ali ndi udindo wosamalira Nyumba ya Ufumu ndipo adzaona kufunika kwake. Zimasangalatsa kwambiri kusonkhana ndiponso kuitanira anthu atsopano mu Nyumba ya Ufumu yosamalidwa bwino.

3 Tiyeneranso kuona mmene Nyumba ya Ufumu yathu ikuonekera. Kodi ikufunika kupakanso penti m’kati kapena kunja? Kodi ikufunika kukonza mwina ndi mwina? Kodi malo oimika magalimoto ndiponso malo ena, akufunika kukonzedwanso? Kodi pali zimene mpingo wanu ungakwanitse kuchita kuti m’kati mwa Nyumba ya Ufumu yanu mukhale mokongola kwambiri? Mungachite zinthu zina zosafuna ndalama zambiri koma zimene zingathandize kuti Nyumba ya Ufumu yanu ikhale yokongola kwambiri. Kumbukirani kuti anthu amalemekeza dzina la Yehova komanso anthu ake ngati Nyumba ya Ufumu imene timasonkhanamo ili yaukhondo, yokongoletsedwa komanso yosamalidwa bwino.—Eks. 35:34, 35; 2 Mbiri 2:11-16.

4 Mmene Nyumba ya Ufumu imagwirira ntchito: Kodi Nyumba ya Ufumu mwini wake ndani? Nyumba ya Ufumu sikhala m’manja mwa mpingo uliwonse. Cholinga cha Nyumba ya Ufumu ndi kulambiriramo Yehova. Mpingo umene unamanga kapena umene umachita lendi Nyumba ya Ufumu, umakhala ndi udindo woisamalira ndipo bungwe la akulu lili ndi udindo woona mmene ikugwiritsidwira ntchito pofuna kuonetsetsa kuti zinthu za Ufumu zikusamalidwa. Ngakhale kuti ofesi ya nthambi polemba makalata imagwiritsa ntchito adiresi ya mpingo umodzi wokha ndiponso Nyumba ya Ufumuyo ingamadziwike ndi dzina la mpingo umenewo, sizitanthauza kuti mpingowo ndi umene uyenera kuika nthawi yoti mipingo yonse imene imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumuyo izisonkhana.

5 Kodi tingatani kuti zimene tingakonze zikhale zokomera mipingo yonse? Mipingo ina imene imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, imaona kuti ndi bwino kuti akulu a mipingo yonseyo azikumana pamodzi pokambirana nkhani zokhudza Nyumba ya Ufumuyo. Zimenezi zimathandiza kuchepetsa mavuto amene amabwera chifukwa chosamvetsetsana. Choncho, mipingo yonse imatha kugwiritsa ntchito nyumba imeneyi yomwe cholinga chake ndi kulambiriramo Yehova. Komanso mpingo uliwonse umakhala ndi udindo woisamalira. Ngati mungatsatire dongosolo limeneli, ndiye kuti palibe mpingo umene ungaone ngati Nyumba ya Ufumuyo ndi yawo kapenanso kuganiza kuti akungochita lendi.—1 Akor. 14:40.

6 Zopereka za Nyumba ya Ufumu: Mpingo uliwonse umene umagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu umafunika kusonyeza kuyamikira popereka ndalama za Nyumba ya Ufumu. Ndalamazi zimathandiza kuti mipingo inanso ikhale ndi Nyumba za Ufumu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena