Tiyeni Tizikonza Malo Athu Olambirirapo
1. Kodi Nyumba ya Ufumu imagwira ntchito yanji?
1 Padziko lonse lapansi pali mipingo ya Mboni za Yehova yopitirira 94,000. Mipingo yambiri imakumana pa Nyumba ya Ufumu, imene ili malo a kulambira koyera ku dera limenelo, kuti iphunzire Baibulo komanso kuti Akristu alimbikitsane.
2. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuonetsetsa kuti Nyumba ya Ufumu izikhala yoyera ndi yooneka bwino?
2 Kukonza Zoyeretsa Nthaŵi ndi Nthaŵi: Ntchito yokonza Nyumba ya Ufumu ndi yofunika kwambiri pa utumiki wathu wopatulika. Buku la Utumiki Wathu pa tsamba 61 limati: “Abale ayenera kuuona kukhala mwayi kuchirikiza Nyumba ya Ufumuyo ndi ndalama komanso kudzipereka pantchito yoisamalira kuti izikhala yaukhondo, yooneka bwino, ndi kukonza moonongeka. M’kati ndi kunja komwe, Nyumba ya Ufumu iyenera kupereka chithunzi choyenerana ndi gulu la Yehova.” Chifukwa chakuti Nyumba ya Ufumu imagwiritsidwa ntchito kangapo mlungu uliwonse, m’pofunika kuti iziyeretsedwa ndi kukonzedwa pafupipafupi. Nthaŵi zambiri anthu a mu mpingo kapena mipingo imene imakumana m’Nyumba ya Ufumuyo amadzipereka kuti achite ntchito imeneyi. Monga mmene zinthu zinaliri mu nthaŵi za m’Baibulo, atumiki a Yehova masiku ano tiyenera kuchita khama “kukonza ndi kulimbitsa” malo athu olambirira.—2 Mbiri 34:10.
3. Kodi ntchito yoyeretsa Nyumba ya Ufumu imalinganizidwa motani, ndipo ndani amene angagwire nawo ntchito imeneyi?
3 Ndandanda yoti azitsatira poyeretsa pa Nyumba ya Ufumu mlungu ndi mlungu iyenera kuikidwa pa bolodi la chidziŵitso. Magulu onse a maphunziro a buku a mpingo ayenera kusinthana poyeretsa Nyumba ya Ufumu mlungu uliwonse, ndipo ayenera kutsatira ndandanda ya zinthu zofunika kuchita akamagwira ntchito yoyeretsayo. Onse amene angathe ayenera kuyeretsa nawo Nyumba ya Ufumu mlungu ndi mlungu kuti izioneka bwino, ndipo umenewu ndi mwayi wapadera. Ana angathandize nawo ngati makolo awo akuwayang’anira, zimene zingawaphunzitse kuti nawonso aziona kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri. Ngati Nyumba ya Ufumuyo imagwiritsidwa ntchito ndi mipingo yoposa umodzi, pamafunika mgwirizano wabwino kuti ntchito yofunika pa kulambira kwathu imeneyi asamangogwira anthu ochepa okha.
4. Kodi payenera kuchitika chiyani kuti mpingo uzidziŵa chochita ukamayeretsa Nyumba ya Ufumu?
4 Mungamate pakhoma ndandanda ya zinthu zofunika kuchita, mwina m’chipinda chimene mumasungiramo zida zogwiritsa ntchito poyeretsa. Ndandanda imeneyi iyenera kufotokoza zinthu zofunika kuchita mlungu uliwonse, monga kupukuta mawindo, kupukuta makauntala, kutaya zinyalala, ndi kukolopa. Ntchito zina zingafunike kumagwiridwa pakapita kanthaŵi, monga kupaka polishi zinthu zonse zamatabwa pamodzinso ndi mipando. Mankhwala otsukira zinthu muyenera kuwaika pamalo poti ana sangafikire ndipo muyenera kulemba dzina lake bwinobwino. Muyeneranso kulemba mwachidule mmene mankhwala alionse angawagwiritsire ntchito.
5. Kodi kupeŵa ngozi n’kofunika motani, ndipo ndi zinthu ziti zimene muyenera kuziona nthaŵi ndi nthaŵi? (Onani bokosi pa tsamba 4.)
5 Kupeŵa ngozi pa Nyumba ya Ufumu n’kofunika kwambiri. (Deut. 22:8) Pa chifukwa chimenechi, bokosi limene lili pa tsamba 4 lili ndi ndandanda ya zinthu zimene muyenera kuziona nthaŵi ndi nthaŵi pofuna kupeŵa ngozi.
6. Kodi ntchito yokonza Nyumba ya Ufumu imayendetsedwa bwanji?
6 Kukonza Zinthu Zimene Zaonongeka pa Nyumba ya Ufumu: Bungwe la akulu lili ndi udindo woyang’anira ntchito yokonza zinthu zoonongeka pa Nyumba ya Ufumu. Nthaŵi zambiri, mkulu kapena mtumiki wotumikira amasankhidwa kuti aziyang’anira ntchito imeneyi. Amakonza mmene zinthu ziyenera kuyendera tsiku ndi tsiku pa Nyumba ya Ufumu, ndipo amaonetsetsa kuti nyumbayo izikhala yoyera komanso yokonzedwa bwino ndiponso amakonza zoti pazikhala zida zokwanira zogwiritsa ntchito poyeretsa. M’pofunika kwambiri kuti m’Nyumba ya Ufumu komanso pabwalo pake pasakhale zinthu zochititsa ngozi. Ngati mipingo iŵiri kapena yoposa pamenepo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mabungwe a akulu amasankha komiti yoti iziona za kasamalidwe ka nyumbayo ndi malowo. Komiti imeneyi imayang’aniridwa ndi mabungwe a akuluwo.
7. (a) Kodi chaka chilichonse n’chiyani chimafunika kuchitika n’cholinga choti Nyumba ya Ufumu ikhale yokonzedwa bwino? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zimafunika kuziona nthaŵi ndi nthaŵi? (Onani bokosi pa tsamba 5.)
7 Nyumba ya Ufumu imafunika kuiyang’ana paliponse ndi kuona mmene ilili kamodzi chaka chilichonse. Akulu ndi amene ali ndi udindo woonetsetsa kuti zinthu zilizonse zimene apeza kuti n’zofuna kukonza zikonzedwe. Ofalitsa angapemphedwe kuti athandizeko pamene pakufunika kukonza. Onse ayenera kuonetsetsa kuti akonze zinthu zonse, kuphatikizapo zinthu zing’onozing’ono ndipo ngati pali zinthu zofunika kukonza azizikonza mwamsanga.
8. Kodi ndi nthaŵi iti pamene akulu angafunse ku ofesi ya nthambi pa nkhani zokhudzana ndi kukonza nyumbayo?
8 Ndi udindo wa mpingo kugwira ntchito yokonza Nyumba ya Ufumu. Komabe, ngati akulu akuona kuti akufunika malangizo kapena thandizo lina pokonza Nyumba ya Ufumuyo, angafunse ku ofesi ya nthambi kuti awathandize. Zina mwa zimene angafunse zingakhale zokhudza kusasuka kwa denga ndi mphepo kapena khoma ndi pansi pa Nyumba ya Ufumu pakakhala ming’alu ikuluikulu.
9. Kodi n’chiyani chimene chimachitika pofuna kuonetsetsa kuti ndalama za mpingo zikugwiritsidwa ntchito moyenera?
9 Kugwiritsa Ntchito Ndalama za Mpingo Mwanzeru: Ntchito yambiri pa Nyumba ya Ufumu ndi pabwalo pake amagwira ndi anthu ongodzipereka. Kudzipereka kwawoko ndi njira yabwino kwambiri yosonyezera chikondi ndipo kumathandiza kwambiri kuchepetsa ndalama zoti zigwiritsidwe ntchito. Ngati pali mipingo yoposa umodzi imene imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumuyo, komiti yoyang’anira Nyumba ya Ufumu izisunga ndalama zapadera. Ndiponso, komitiyo izilemba ndi kupereka lipoti la mmene ndalamazo zagwiritsidwira ntchito mwezi uliwonse ku bungwe la akulu lililonse, n’cholinga choti akuluwo azidziŵa mmene ndalamazo zikugwiritsidwira ntchito. Akulu ali ndi udindo woonetsetsa kuti ndalama za mpingo zikugwiritsidwa ntchito moyenera.
10. Kodi n’chiyani chimene chiyenera kuchitika ngati pakufunika ntchito yaikulu yokonza moonongeka?
10 Ntchito Yaikulu Yokonza Moonongeka: Komiti yoyang’anira Nyumba ya Ufumu ikaona kuti pakufunika ntchito yaikulu yokonza Nyumba ya Ufumuyo kapena yokhudzana ndi kayendetsedwe kake, imafotokoza zimenezi kwa bungwe la akulu kuti liwauze chochita. Ngati aona kuti pakufunika ntchito yaikulu yokonza moonongeka kapena ngati pakufunika kuti anthu ena kupatulapo anthu a mu mpingo kapena mipingo imene imasonkhana m’Nyumba ya Ufumuyo athandizepo, akulu angafunse ku ofesi ya nthambi. A ku ofesi ya nthambiwo amapereka mfundo zothandiza komanso amayang’anira ndi kutsogolera ntchitoyo. Ngati pakufunika kugula zinthu za ndalama zambiri, m’pofunika kuti afufuze mtengo wolondola ndiyeno alembe chigamulo choti mpingo uvomereze.—Onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 1994.
11. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mwayi wathu wapadera wosonkhana pa Nyumba ya Ufumu?
11 Timayamikira kwambiri mwayi wathu wapadera wosonkhana pa Nyumba ya Ufumu! Sitingafune kunyalanyaza misonkhano yathu kapena kuiona ngati yopanda phindu. Onse angathandize kuti misonkhano imene imatilimbikitsayi iziyenda bwino mwa kuchita nawo zonse zimene angathe posamalira Nyumba ya Ufumu. Zimenezi zimalemekeza kulambira koyera ndipo zimapereka ulemu ku dzina la Yehova. Choncho, tiyeni tiziyesetsa kukonza malo athu olambirira.
[Bokosi patsamba 4]
Zinthu Zofunika Kuziona Kuti Mupeŵe Ngozi
◻ Chipinda chochitiramo sukulu ya utumiki wa Mulungu yachiwiri, zipinda zosungiramo katundu (ngati zilipo), zimbudzi, ndi zipinda zosungiramo zovala ziyenera kukhala zoyera. Zinthu zimene zili m’menemo zikhale zolongedzedwa bwino, musakhale zinyalala, ndiponso musakhale chinthu chilichonse chimene chingagwire moto kapena zinthu zanuzanu osati za pa Nyumba ya Ufumuyo.
◻ Denga, magata (ngati alipo) ndi ngalande zodutsa madzi a mvula ziyenera kuonedwa ndi kuyeretsedwa nthaŵi ndi nthaŵi.
◻ M’tinjira ndi malo oimikapo magalimoto musamakhale zinthu zimene zingapangitse kuti munthu aterereke kapena agwe.
◻ Denga likamadontha kapena mapaipi a madzi akamachucha m’kati mwa nyumbayo ayenera kukonzedwa mwamsanga kuti mupeŵe vuto la chinyezi.
◻ Nyumbayo iyenera kutsekedwa ndi makiyi ngati pamalopo palibe munthu wina aliyense.
◻ Onetsetsani kuti mabenchi ndi olimba ndipo akonzedwa ngati pakufunika kutero.
◻ Tayani zinthu zonse zosafunikira.
◻ Msonkhano uliwonse ukatha chinthu chilichonse cha mtengo wapatali chimene munthu angathe kuba muzichichotsa m’Nyumba ya Ufumuyo ndipo muzichotsa ndalama m’mabokosi a zopereka.
◻ Zinthu zonse zogwiritsira ntchito pokonza Nyumba ya Ufumu monga penti, simenti, laimu, ndi zina zotero musamazisiye pa nyumbayo.
[Bokosi patsamba 5]
Kusamalira Nyumbayo ndi Malowo
◻ Kunja kwa nyumbayo: Kodi denga, makoma, penti, mawindo ndi chikwangwani cha Nyumba ya Ufumu zili bwino?
◻ Pabwalo: Kodi pabwalo m’posamalidwa bwino? Kodi mitengo ndi yodulira bwino, ndipo kodi maluwa ndi opalilidwa bwino?
◻ Mkati: Ngati pali makatani, mipando, zida zamagetsi ndi zamadzi, kodi zili bwino? Kodi mabenchi akuoneka bwino? Kodi makabati osungamo mabuku amatheka kuwatseka ndi makiyi? Kodi sitandi ya wokamba nkhani ili bwino? Kodi mumakolopa m’nyumbayo pafupipafupi?
◻ Zipangizo: Ngati muli ndi magetsi ndi zida zokuzira mawu, kodi zikugwira ntchito bwinobwino?
◻ Zimbudzi: Kodi n’zaukhondo ndipo kodi zikugwira ntchito bwinobwino? Ngati muli ndi zimbudzi zokumba kodi mumavundikirapo kuti mupewe ntchentche? M’tauni mmene muli zimbudzi za madzi, kodi thanki ndi pokhalira pake zili bwino?
◻ Makalata a mpingo: Kodi ndandanda ya zinthu zofunika kukonza mwaiika pa bolodi la chidziŵitso? Kodi mwachitanso chimodzimodzi ndi ndandanda yoyeretsera ya mpingo?
◻ Musamasunge m’Nyumba ya Ufumu katundu kapena zida zimene zatsala pomanga kapena pokonza nyumbayo.