Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • od mutu 11 tsamba 116-122
  • Malo Olambirira Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malo Olambirira Yehova
  • Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • NYUMBA YA UFUMU
  • KUMANGA NYUMBA ZA UFUMU
  • MALO A MISONKHANO
  • Kodi Nyumba ya Ufumu Yanu Mumaiona Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Tizilemekeza Malo Athu Olambirira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tiyeni Tizikonza Malo Athu Olambirirapo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Kodi Mumalemekeza Malo Anu Olambirira?
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
od mutu 11 tsamba 116-122

MUTU 11

Malo Olambirira Yehova

OLAMBIRA oona a Yehova analamulidwa kuti azisonkhana n’cholinga choti azilandira malangizo komanso azilimbikitsana. (Aheb. 10:23-25) Malo oyamba osonkhanira amene Aisiraeli, omwe anali anthu osankhidwa ndi Mulungu, ankagwiritsa ntchito anali “chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako.” (Eks. 39:32, 40) Patapita nthawi, Solomo mwana wa Davide anamanga nyumba, kapena kuti kachisi, ndipo anachita zimenezi pofuna kulemekeza Mulungu. (1 Maf. 9:3) Kachisi ameneyu atawonongedwa mu 607 B.C.E., Ayuda anayamba kusonkhana m’nyumba zina zomwe ankazitchula kuti masunagoge kuti azilambira Mulungu. Patapita nthawi, kachisi uja anamangidwanso ndipo anayambiranso kugwiritsidwa ntchito monga likulu la kulambira koona. Ndipo Yesu analalikirapo m’masunagoge komanso m’kachisi. (Luka 4:16; Yoh. 18:20) Nthawi inanso anachititsa msonkhano paphiri.​—Mat. 5:1–7:29.

2 Yesu atamwalira, Akhristu anayamba kusonkhana m’nyumba zomwe zinkagwiritsidwanso ntchito zina komanso ankasonkhana m’nyumba za anthu kuti aphunzitse Malemba ndiponso kuti alimbikitsane ndi okhulupirira anzawo. (Mac. 19:8, 9; Aroma 16:3, 5; Akol. 4:15; Filim. 2) Nthawi zina Akhristu oyambirira ankafunika kusonkhana pamalo oti anthu ena asadziwe poopa kuzunzidwa. Izi zikusonyeza kuti atumiki a Mulungu okhulupirika akale ankafunitsitsa kupezeka pamalo olambirira n’cholinga choti ‘aphunzitsidwe ndi Yehova.’​—Yes. 54:13.

3 Masiku anonso misonkhano yachikhristu imatha kuchitika m’maholo wamba kapena m’nyumba za anthu. Nyumba za anthu zimagwiritsidwa ntchito kwambiri pochitiramo misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda. Anthu amene amalola kuti nyumba zawo zizigwiritsidwa ntchito pochitira misonkhano imeneyi amaona kuti ndi mwayi waukulu kuti nyumba yawo imagwiritsidwa ntchito mwanjira imeneyi. Ambiri amaona kuti apindula kwambiri mwauzimu chifukwa cholola kuti nyumba yawo izigwiritsidwa ntchito ngati malo osonkhanira.

NYUMBA YA UFUMU

4 Nyumba ya Ufumu ndi malo amene Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito kwambiri pochita misonkhano ya mpingo. Nthawi zambiri zimene zimachitika ndi zakuti, timagula malo n’kumangapo Nyumba ya Ufumu yatsopano kapena timagula nyumba yomangamanga n’kuikonza kuti ikhale Nyumba ya Ufumu. Zikakhala zotheka, pofuna kuti tisawononge ndalama zambiri komanso kuti nyumbazi zisamapezeke kuti zikungokhala, mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi. Koma m’madera ena zimakhala bwino kungochita lendi holo inayake. Pakamangidwa Nyumba ya Ufumu yatsopano kapena zinthu zikuluzikulu za pa Nyumba ya Ufumu yakale zikakonzedwa, zimakhala zoyenera kukamba nkhani yopereka nyumbayo kwa Yehova. Koma ngati nyumbayo yangokonzedwa pang’ono, palibe chifukwa chokhalira ndi msonkhano wopereka nyumbayo kwa Yehova.

5 Nyumba ya Ufumu isamamangidwe mwanjira yongofuna kugometsa anthu. Ngakhale kuti maonekedwe a Nyumba ya Ufumu angasiyane potengera madera, nthawi zonse cholinga chake ndi kulambiriramo Yehova. (Mac. 17:24) Malinga ndi mmene zinthu zilili kumaloko, Nyumba ya Ufumu iyenera kukhala yotakasuka komanso yabwino kuchitiramo misonkhano yachikhristu.

6 Mipingo yonse ya Mboni za Yehova imathandiza pokonza komanso kusamalira Nyumba ya Ufumu imene amagwiritsa ntchito. Iwo sayendetsa mbale ya zopereka kapena kupemphetsa ndalama pa misonkhano yawo. Mu Nyumba ya Ufumu mumakhala bokosi la zopereka n’cholinga choti amene abwera kumisonkhano aponyemo zopereka zawo ngati akufuna kuthandiza nawo kulipira zinthu zofunika za pa nyumbayo. Anthu amapereka ndalamazi mwakufuna kwawo komanso mochokera pansi pa mtima.​—2 Akor. 9:7.

7 Anthu onse mumpingo amaona kuti ndi mwayi kupereka ndalama zothandizira pa Nyumba ya Ufumu komanso kudzipereka kugwira nawo ntchito yosamalira nyumbayo. Nthawi zambiri pamasankhidwa mkulu kapena mtumiki wothandiza woti azilemba ndandanda yosamalira nyumbayo. M’mipingo yambiri, ntchito yoyeretsa Nyumba ya Ufumu imagawidwa potsatira timagulu ta utumiki wakumunda ndipo woyang’anira kagulu kapena wothandiza wake ndi amene amatsogolera pogwira ntchitoyo. Maonekedwe a mkati ndi kunja kwa Nyumba ya Ufumu ayenera kulemekezetsa Yehova ndi gulu lake.

Anthu onse mumpingo amaona kuti ndi mwayi kupereka ndalama zothandizira pa Nyumba ya Ufumu komanso kudzipereka kugwira nawo ntchito yosamalira nyumbayo

8 Ngati Nyumba ya Ufumu imodzi imagwiritsidwa ntchito ndi mipingo ingapo, akulu a mipingo yonseyo amasankha Komiti Yoyang’anira Nyumba ya Ufumu, imene imayang’anira ntchito yosamalira nyumbayo komanso katundu. Mabungwe a akuluwo amasankha m’bale mmodzi kuti akhale wogwirizanitsa komitiyo. Motsogoleredwa ndi mabungwe onse a akulu, komitiyi imayang’anira ntchito yoyeretsa nyumbayo, kukonza mmene mwawonongeka ndiponso kuonetsetsa kuti zinthu zofunikira posamalira nyumbayo zilipo zokwanira. Kuti ntchito imeneyi iyende bwino, pamafunika kuti mipingo yonse izichita zinthu mogwirizana.

9 Ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, iyenera kumasinthana nthawi yoyambira misonkhano. Akulu ayenera kukambirana mwachikondi komanso moganizirana pamene akusankha nthawi imene mpingo uliwonse ukhoza kumachita misonkhano yake. (Afil. 2:2-4; 1 Pet. 3:8) Palibe mpingo umene uli ndi mphamvu yosankhira mipingo ina nthawi yochitira misonkhano. Ngati mpingo umodzi umene umagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumuyo ukuchezeredwa ndi woyang’anira dera, mipingo inayo iyenera kusintha nthawi yawo ya misonkhano mlungu umenewo.

10 Nyumba ya Ufumu ingagwiritsidwe ntchito pokambiramo nkhani ya ukwati kapena ya maliro ngati Komiti ya Utumiki ya Mpingo yavomereza zimenezi. Munthu akapempha kuti akufuna kugwiritsa ntchito nyumbayo, abale amenewa amaiganizira nkhaniyo mofatsa n’kusankha zoyenera kuchita malinga ndi malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi.

11 Anthu amene amapatsidwa mwayi wogwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu kuti akambiremo nkhani ya ukwati kapena ya maliro ayenera kuchita zinthu mosonyeza kuti ali pamalo olambirirapo Yehova. Pa Nyumba ya Ufumu sipayenera kuchitika chilichonse chomwe chingakhumudwitse kapena kuipitsa mbiri ya mpingo kapenanso kunyozetsa dzina la Yehova. (Afil. 2:14, 15) Nthawi zina ofesi ya nthambi ingakonze zoti Nyumba ya Ufumu igwiritsidwe ntchito kuchitirapo zinthu zina zauzimu, monga Sukulu ya Utumiki wa Ufumu kapena Sukulu ya Utumiki Waupainiya.

12 Nthawi zonse mpingo uyenera kulemekeza malo awo osonkhana. Kavalidwe kathu, mmene timadzikongoletsera komanso khalidwe lathu, ziyenera kusonyeza kuti timalambira Yehova. (Mlal. 5:1; 1 Tim. 2:9, 10) Tikamatsatira malangizo amenewa timasonyeza kuti timayamikira misonkhano yathu yachikhristu.

13 Pa nthawi ya misonkhano sipafunika kukhala zosokoneza zilizonse. Choncho ndi bwino kuti makolo azikhala limodzi ndi ana awo. Makolo amene ali ndi ana aang’ono ayenera kulimbikitsidwa kukhala malo amene sangasokoneze kwambiri anthu ngati atafuna kutuluka ndi anawo kuti akawalange kapena kuti akawasamalire.

14 Abale oyenerera amasankhidwa kuti azilandira alendo pa Nyumba ya Ufumu. Ayenera kukhala atcheru, ansangala ndiponso otha kudziwa zoyenera kuchita ngati patachitika zinthu zadzidzidzi. Ntchito zawo zimaphatikizapo kulandira alendo, kuthandiza anthu obwera mochedwa kupeza malo okhala, kulemba chiwerengero cha osonkhana ndiponso kuonetsetsa kuti m’Nyumba ya Ufumu mukulowa mpweya wokwanira. Nthawi zina amathandizanso makolo kuti azisamalira ana awo kuti asamathamangethamange misonkhano isanayambe kapena ikangotha komanso kuti asamakasewere kupulatifomu. Wolandira alendo akhoza kupempha mwaulemu komanso mwanzeru makolo a mwana amene akuvutitsa kuti atuluke naye n’cholinga choti asasokoneze ena. Ntchito imene olandira alendo amagwira imathandiza kwambiri kuti aliyense apindule ndi misonkhano. Zimakhala bwino kuti olandira alendowa akhale akulu komanso atumiki othandiza.

KUMANGA NYUMBA ZA UFUMU

15 M’nthawi ya atumwi, Akhristu ena anali opeza bwino kuposa anzawo, n’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndikufuna kuti zochuluka zimene muli nazo zithandizire pa zimene iwowo akusowa, ndipo zochuluka zimene iwowo ali nazo zithandizire pa zimene inuyo mukusowa, kuti pakhale kufanana.” (2 Akor. 8:14) Masiku anonso timayesetsa kuti “pakhale kufanana.” Ndalama zimene mipingo imapereka padziko lonse lapansi zimaphatikizidwa pamodzi kuti zizithandiza pa ntchito yomanga ndiponso kukonza Nyumba za Ufumu. Gulu lathu komanso mipingo imene imathandizidwa ndi ndalamazi, imayamikira kwambiri kuwolowa manja kwa abale ndi alongo apadziko lonse.

16 Ofesi ya nthambi ndi imene imagawira mipingo Nyumba ya Ufumu yoti izisonkhana ndipo pamakhala zinthu zingapo zimene amaganizira asanachite zimenezi. Ofesi ya nthambi ndi imenenso imasankha malo oyenera kumanga Nyumba za Ufumu zatsopano kapena kukonza Nyumba za Ufumu zakale zimene zili m’gawo la nthambi yawo. Pakachitika ngozi zadzidzidzi, ofesi ya nthambi imakonza zoti Nyumba za Ufumu zikonzedwe ndipo nthawi zina amakonzanso nyumba za abale.

17 Ofesi ya nthambi ndi imene imatsogolera ntchito imene anthu ongodzipereka amagwira. Anthuwa amagula malo, kulemba pulani, kukapeza chilolezo kuboma, ndiponso kugwira ntchito yomanga ndi kukonzanso zowonongeka. Popeza m’mayiko ambiri mukufunika Nyumba za Ufumu, gulu likufuna anthu ambiri omwe angadzipereke kugwira ntchitoyi. Ofalitsa obatizidwa amene akufuna kuthandiza nawo pa ntchito yomanga, ayenera kulemba fomu yofunsira utumikiwu n’kuipereka ku Komiti ya Utumiki ya Mpingo wawo. Ndipo ofalitsa osabatizidwa angathe kuthandiza nawo pa ntchito yomanga kapena kukonza Nyumba ya Ufumu yawo.

MALO A MISONKHANO

18 Nthawi zambiri Akhristu oyambirira ankasonkhana m’timagulu ting’onoting’ono. Komabe nthawi zina “anthu ambirimbiri” ankasonkhana pamodzi. (Mac. 11:26) Masiku anonso anthu ambirimbiri a Yehova amasonkhana pa nthawi ya misonkhano yadera ndiponso yachigawo. Nthawi zambiri timangochita lendi malo a m’deralo, koma ngati malo abwino palibe, timamanga malo olambirira amene timawatchula kuti Malo a Msonkhano (m’mayiko ena kumamangidwa Nyumba za Misonkhano).

19 Nthawi zina ofesi ya nthambi imagula nyumba yomangamanga n’kungoikonza kuti ikhale Nyumba ya Msonkhano. Koma nthawi zambiri amangogula malo n’kumanga Nyumba ya Msonkhano kapena Malo a Msonkhano. Malo a Misonkhano amakhala aakulu mosiyanasiyana potengera ndi mmene zinthu zilili m’deralo. Ofesi ya nthambi imagula kapena kumanga Malo a Msonkhano pambuyo powerengera ndalama zimene zingafunikire ndiponso kuganizira kuti malowo azidzagwiritsidwa ntchito kangati pa chaka.

20 Ofesi ya nthambi imasankha abale oti azisamalira malowa. Pamakonzedwa zoti mipingo ya m’deralo izikayeretsa malowa nthawi ndi nthawi komanso kukakonza zina ndi zina. Zimakhala bwino kwambiri abale akamadzipereka kukagwira ntchitoyi. Choncho mipingo ikulimbikitsidwa kuthandiza nawo pa ntchito imeneyi ndi mtima wonse.​—Sal. 110:3; Mal. 1:10.

21 Nthawi zina Nyumba za Misonkhano zimagwiritsidwa ntchito pa zinthu zina zauzimu monga Sukulu Zophunzitsa Baibulo ndiponso misonkhano yapadera ya oyang’anira madera. Mofanana ndi Nyumba za Ufumu, cholinga cha Malo a Misonkhano ndi kulambirirapo Yehova. Tikakhala pa Malo a Msonkhano, zochita zathu, mmene tavalira ndiponso mmene tadzikongoletsera zizikhala zaulemu ngati mmene timachitira tikakhala pa Nyumba ya Ufumu.

22 M’masiku otsiriza ano, anthu ambiri atsopano akufunitsitsa kulowa m’gulu la Yehova. Uwu ndi umboni wakuti Yehova akutidalitsa. (Yes. 60:8, 10, 11, 22) Choncho tiyenera kuthandiza nawo pa ntchito yomanga, kukonza ndiponso kusamalira malo olambirira. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timaona kuti malo amenewa ndi ofunika kwambiri, chifukwa n’kumene timasonkhana kuti tizilimbikitsana makamaka pamene tsiku la Yehova likuyandikira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena