Kodi Mumalemekeza Malo Anu Olambirira?
“Kuyambira pachiyambi penipeni pa uthenga wabwino, nthaŵi zonse Akristu anali ndi malo okhazikika ndi otsimikizirika olambirira Mulungu.”—“Primitive Christianity,” lolembedwa ndi William Cave.
NTHAŴI zonse anthu a Mulungu asangalala kusonkhana pamodzi kaamba ka kulambira. Zimenezi zinali zowona m’zaka za zana loyamba monga momwe ziliri tsopano. Alembi ndi akatswiri amaphunziro azaumulungu oyambirira, monga ngati Lucian, Clement, Justin Martyr, ndi Tertullian, onse amavomereza kuti Akristu anali ndi malo akutiakuti kumene anasonkhana kulambira pamodzi mokhazikika.
Baibulo limafotokoza mfundo imodzimodziyo, likumapereka maumboni ambiri onena za misonkhano yokhazikika yochitidwa ndi magulu a Akristu. Magulu ameneŵa anali kudziŵika monga mipingo. Zimenezi zinali zoyenera chifukwa chakuti dzina lakuti “mpingo” m’zinenero zoyambirira za Baibulo limatanthauza gulu la anthu osonkhana pamodzi kaamba ka chifuno kapena ntchito yakutiyakuti.
Malo Oyambirira a Kulambira Kwachikristu
Kodi Akristu a m’zaka za zana loyamba anachitanji pamene anasonkhana pamodzi? Baibulo limafotokoza ingapo ya misonkhano imeneyo ndipo limasonyeza kuti kuphunzitsa kunali mbali yofunika. (Machitidwe 2:42; 11:26; 1 Akorinto 14:19, 26) Maprogramu akuphunzira anakonzedwa, okhala ndi nkhani, kusimba zokumana nazo zolimbikitsa, ndi kukambitsirana mosamalitsa makalata olandiridwa kuchokera kubungwe lolamulira ku Yerusalemu kapena kwa mtumwi.
Pa Machitidwe 15:22-35, timaŵerenga kuti pambuyo pakuŵerengedwa kwa kalata imodzi yoteroyo imene inatumizidwa ku kagulu ka Akristu a ku Antiokeya, Yuda ndi Sila “anasangalatsa abale ndi mawu ambiri, nawalimbikitsa.” Mbiri ina imanena kuti pamene Paulo ndi Barnaba anafika ku Antiokeya “nasonkhanitsa mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nawo.” Kupemphera kwa Yehova kunalinso mbali yofunika ya misonkhano Yachikristu.—Machitidwe 14:27.
Malo amene mipingo ya m’zaka za zana loyamba inasonkhanako kaamba ka kulambira sizinali nyumba zokongoletsedwa mopambanitsa mofanana ndi matchalitchi ambiri a Chikristu Chadziko lerolino. Kwakukulukulu, Akristu oyambirira anasonkhana m’nyumba za anthu. (Aroma 16:5; 1 Akorinto 16:19; Akolose 4:15; Filemoni 2) Kaŵirikaŵiri chipinda chapamwamba cha nyumba ndicho chinali kugwiritsiridwa ntchito. Munali m’chipinda chapamwamba mmene Mgonero wa Ambuye unachitidwira. Munalinso m’chipinda chapamwamba mmene ophunzira 120 anadzozedwa ndi mzimu woyera pa Pentekoste.—Luka 22:11, 12, 19, 20; Machitidwe 1:13, 14; 2:1-4; 20:7, 9.
Lerolino Mboni za Yehova zimatsatira njira yokhazikitsidwa ndi atumwi. Izo zimagwiritsira ntchito malo osonkhanira odziŵika monga Nyumba Zaufumu. Kumeneko zimaphunzitsidwa kukhala alaliki a mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Panyumba Yaufumupo, izo zimaphunziranso Malemba, kupemphera, ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake. Zimenezi nzogwirizana ndi uphungu wa Baibulo wopezeka pa Ahebri 10:24, 25 pamene pamati: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muwona tsiku lilikuyandika.”
Kugwiritsira Ntchito Malo Athu Olambirira Moyenera
Kodi mukukumbukira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere” ndiakuti, “Zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka”? Mutapenda mawu apatsogolo ndi apambuyo a mawu amenewo, mudzawona kuti Paulo anali kulankhula za mmene misonkhano Yachikristu iyenera kuchitidwira. Mofanana ndi m’nyengo ya atumwi, Akristu lerolino amatsimikiza kuti misonkhano yawo njadongosolo ndi yolinganizidwa bwino.—1 Akorinto 14:26-40.
Kope la The Watchtower la October 15, 1969 linanena kuti: “Mkhalidwe wauzimu umene umakhala pa Nyumba Yaufumu uli weniweni, wochititsidwa ndi chikondwerero chenicheni cha kulambira kowona ndi malangizo a Baibulo. Ndipo kukometseredwa kwachikatikati ndi kwachibadwa m’nyumbayo kumasonkhezera amene alimo kukhala aubwenzi, osaletsedwa ndi dzoma losadziŵika.” Ndithudi, chisamaliro chimaperekedwanso kuwona kuti nthaŵi zonse Nyumba Yaufumu imagwiritsiridwa ntchito mwaulemu.
Chikristu Chadziko chasonyeza kupanda ulemu kwakukulu pankhani imeneyi. Magulu ena achipembedzo amagwiritsira ntchito malo awo olambirira monga malo azamaseŵera. Iwo amakhala ndi makonsati a nyimbo za rock zachipembedzo, malo ochitira maseŵera onyamula zolemera, magome oseŵerera mpira, sukulu za mkaka, ndi akanema. Tchalitchi china chinali ndi mpikisano wa maseŵera olimbana monga mbali ya programu yake. Zimenezi sizimagwirizana konse ndi dongosolo limene atumwi anaika.
Ngati mpingo uliwonse wa m’zaka za zana loyamba unachita mosayenera, unafunikira kuwongoleredwa. Mwachitsanzo, anthu ena mumpingo Wachikristu wa ku Korinto anali kugwiritsira ntchito phwando la Mgonero wa Ambuye monga nthaŵi yakudya ndi kumwa. Iwo anali kubweretsa chakudya chawo chamadzulo kuti adzadye msonkhanowo usanayambe kapena uli mkati, ena anadya ndi kumwa mopambanitsadi. Zimenezi zinalidi zosayenera. Mtumwi Paulo anawalembera kuti: “Nanga mulibe nyumba zakudyeramo ndi kumweramo?”—1 Akorinto 11:20-29.
Mogwirizana ndi uphungu wa Paulo, Mboni za Yehova zimayesayesa kuchitira zinthu zaumwini kunyumba kapena kumalo ena osati ku Nyumba Yaufumu. Zowona, misonkhano yathu yokhazikika imatipatsa mpata wabwino wa kuwona mabwenzi ambiri panthaŵi imodzi. Komabe, Nyumba Yaufumu njopatulidwira Yehova, chotero iyenera kugwiritsiridwa ntchito kaamba ka kulambiridwa kwake kokha. Sitimagwiritsira ntchito mwaŵi wathu wa kupezekapo kulondola zinthu zakudziko kapena kuchita malonda athu.
Ndiponso, Nyumba Zaufumu sizimagwiritsiridwa ntchito ndi mpingo kuchitiramo zosangulutsa, machitachita osonkhetsa ndalama, kapena mautumiki achitaganya, monga ngati kulererako ana. Kuli malo ena kumene munthu angachitire zinthu zaumwini ndi zamalonda zimenezo.
Akulu pa Nyumba Yaufumu ina anawona kuti ziŵalo za mpingo zinali kuchita chizoloŵezi cha kubwereka kapena kubweza zinthu zobwerekedwa pamisonkhano. Ndiponso, iwo anali ndi chizoloŵezi cha kusinthana akanema apakaseti ya vidiyo pa Nyumba Yaufumu. Ngakhale kuti zochitikazo sizinali za malonda, akuluwo anawathandiza kuwona ubwino wa kuchitira zinthu zimenezo kunyumba pamene kuli kotheka.
Pofuna kupeŵa mikhalidwe imene ikapereka lingaliro lolakwa ndi kutsimikizira kuti Nyumba Yaufumu ikugwiritsiridwa ntchito moyenera, munthu aliyense ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi pali zinthu zina zaumwini zimene ndakhala ndikuchitira ku Nyumba Yaufumu zimene ndikanachitira kunyumba?’ Mwachitsanzo, pamene mukupanga makonzedwe opita kocheza kapena kusonkhana kwamayanjano kwina, kodi sikukakhala kwabwinopo kukambitsirana za makonzedwe amenewo kunyumba? Kodi tingagwiritsire ntchito lamya kapena kupita kunyumba za amene tikufuna kulankhula nawo? Titagwiritsira ntchito mawu a Paulo, tingakhoze kunena kuti: ‘Nanga tilibe nyumba za kusamalira nkhani zoterozo?’
Nthaŵi ndi Malo Zoikidwiratu Zolambirira Yehova
Baibulo limanena pa Mlaliki 3:1 kuti: “Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake.” Pamene tili pamisonkhano pa Nyumba Yaufumu, tingadziloŵetse kotheratu m’zinthu zimene zimagwirizana ndi utumiki wathu Wachikristu. Ndinthaŵi yoikidwiratu ya kulambira Yehova.
Yakobo, mbale wa Yesu mwa bambo wina anapereka uphungu pankhani ya tsankho mumpingo Wachikristu. (Yakobo 2:1-9) Kodi tingagwiritsire ntchito motani uphungu umenewu m’Nyumba Zaufumu zathu? Pangawonekere kukhala tsankho ngati tipereka mobisa makalata oitanira ena ku zochitika zamayanjano kumeneko. Mumpingo wina munali chizoloŵezi choika makalata oitanirawo m’zikwama kapena m’Mabaibulo a amene alipowo. Zowona, zimenezi nzokhweka kuposa kutumiza makalatawo papositi kapena kukawapereka nokha kunyumba iliyonse. Komabe, kodi amene salandira makalatawo amamva motani pambuyo powona makalatawo akuperekedwa kwa anthu ena? Kodi zimenezi zingasonyeze tsankho?
Ndithudi, sipafunikira kukhala lamulo lokhwima lonena kuti palibe munthu wina amene ayenera kupereka uthenga kapena katundu wake kwa munthu wina pa Nyumba Yaufumu; ndiponso sikolakwa kulankhula m’Nyumba Yaufumu ponena za zinthu kapena zochitika zatsiku ndi tsiku, kuitana munthu wina kudzacheza kunyumba kwanu, kapena kupempha munthu wina kuti atsagane nanu kupita kokasanguluka. Koma zimenezi ziyenera kukhala zakamodzikamodzi ndipo ziyenera kuchitidwa mochenjera ndi mosapupuluma. Makonzedwe aumwini sayenera konse kucheukitsa chifuno chenicheni cha kusonkhana kwathu pa Nyumba Yaufumu, chija chakulimbikitsidwa mwauzimu.—Mateyu 6:33; Afilipi 1:10.
Amuna Amene Amapereka Chitsanzo
Akulu ndi atumiki otumikira mwachangu amapereka chitsanzo m’kusonyeza ulemu pa Nyumba Yaufumu. Nthaŵi zambiri pamakhala mkulu mmodzi kapena aŵiri ndi atumiki otumikira amene amagaŵiridwa kuyang’anira nkhani zokhudza kusamalira Nyumba Yaufumu. Kumene mipingo yambiri imagwiritsira ntchito nyumba imodzimodziyoyo, komiti ya akulu imayang’anira nkhani zimenezi.
Pamene kuli kwakuti anthu ena amagaŵiridwa mwachindunji kuyang’anira mathayo amenewo, atumiki otumikira ndi akulu onse ayenera kusonyeza chikondwerero chenicheni ndi nyumbayo. Iwo amazindikira kuti Nyumba Yaufumuyo yapatulidwira Yehova ndipo imagwiritsiridwa ntchito kaamba ka kulambiridwa kwake.
Akulu sayenera kuzengereza pamene nyumbayo ifunikira kukonzedwa. (2 Mbiri 24:5, 13; 29:3; 34:8; Nehemiya 10:39; 13:11) M’mipingo ina Nyumba Yaufumu imapendedwa nthaŵi ndi nthaŵi kotero kuti chisamaliro chamwamsanga chiperekedwe kukonza moonongeka. Chiŵerengero cha zinthu zogwiritsira ntchito chimasungidwa kutsimikizira kuti zinthu zofunika zilipo. Ngati pali malo akutiakuti osungira katundu, zipangizo, ndi ziŵiya zoyeretsera, akulu ndi atumiki otumikira onse ayenera kusonyeza chikondwerero m’kawonekedwe kake, akumatsimikizira kuti malowo ngaudongo. Amene amagwira ntchito pamalo ogulitsira mabuku ndi magazini angasonyeze chikondwerero chawo mwakutsimikizira kuti makatoni opanda kanthu sakusiidwa paliponse m’nyumbayo.
Mwakukhazikitsa chitsanzo, akulu ndi atumiki otumikira angathandize mpingo wonse kusonyeza changu cha Nyumba Yaufumu. (Ahebri 13:7) Onse angasonyeze ulemu woyenera mwakukhala ndi phande kuyeretsa nyumbayo ndi mwakusonyeza chikondwerero chenicheni mwakusamalira kawonekedwe kake.
Yesu ananena pa Mateyu 18:20 kuti: “Kumene kuli aŵiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndili komweko pakati pawo.” Inde, Yesu amakondwera ndi zimene timachita pamene tisonkhana pamodzi kudzalambira Yehova. Zimenezi zimaphatikizapo misonkhano iliyonse yochitidwa m’nyumba za anthu ndi misonkhano yaikulu monga ngati misonkhano yachigawo ndi yadera.
Kwa mamiliyoni a Mboni za Yehova, palibe malo ena amene ali apamtima kwambiri kuposa malo awo okhazikika olambirira, Nyumba Yaufumu. Izo zimasonyeza ulemu woyenera pamalowo. Izo zimasonyeza mzimu wakhama poisamalira, ndipo nthaŵi zonse zimayesayesa kuigwiritsira ntchito moyenera. Nanunso tsatiranitu uphungu umene Yehova iyemwini amapereka wakuti: “Samalira phazi lako popita ku nyumba ya Mulungu.”—Mlaliki 5:1.