Kodi Mukanena Chiyani kwa Munthu Wachiyuda?
1 M’zaka za zana loyamba, “ana a Aisrayeli” ambiri analabadira moyamikira kulalikira kwa Yesu ndi ophunzira ake. (Mac. 10:36) Monga mmene zinalili nthaŵiyo, lerolinonso Ayuda ambiri oona mtima akuphunzira choonadi mofunitsitsa—osati kokha ku Israyeli komanso ku Russia, United States ndi m’mayiko ena. Kodi mukufuna kukhala wogwira mtima pochitira umboni anthu achiyuda? Malingaliro otsatirawa adzakuthandizani kupereka umboni mwaluso kwa Ayuda opembedza ndi osapembedza omwe.
2 Kuchitira Umboni kwa Ayuda Opembedza: Muyenera kudziŵa kuti kaŵirikaŵiri Ayuda opembedza amakonda kwambiri miyambo ya arabi kusiyana ndi kuyesa kufotokoza ziphunzitso zakutizakuti. N’zoona kuti ambiri amaona mwambo kukhala wamphamvu mofanana ndi Malemba. Chotero, sasangalala kukambirana nkhani zakuya za m’Baibulo. Ndipo amaona Baibulo kukhala buku la Akristu. Chifukwa cha chimenecho, nthaŵi zambiri pofuna kugwiritsa ntchito Baibulo ndi bwino kutchula mawu ngati “Malemba Achihebri,” “Tora,” kapena “Malemba.”
3 Ndi mitu iti imene ingakope chidwi Ayuda opembedza? Eya, iwo amakhulupirira kuti pali Mulungu mmodzi, amene amakonda anthu. Amakhulupiriranso kuti Mulungu amaloŵerera m’nkhani za anthu. Mungagwiritsire ntchito mfundo zimenezi kuti mugwirizane. Komanso, Ayuda ambiri akudziŵa bwino mmene abale awo anavutikira mu Nkhondo Yachiŵiri Yapadziko Lonse. Amafunsa chifukwa chake Mulungu analola kusalungama kumeneku ndi nthaŵi imene kuipa kudzatha. Ndife okonzekera bwino kuyankha mafunso otereŵa, mwachitsanzo, kuchokera m’zimene abale athu anakumana nazo panthaŵi imene a Nazi ankapululutsa anthu.
4 Ndithudi, popeŵa kukwiyitsa mwininyumba, ndi bwino kusaloŵetsamo nkhani yodziŵikitsa Mesiya mofulumira m’makambiranowo. M’malo mwake, mungakambirane zimene Mose anachita m’mbiri ya Israyeli ndiyeno funsani mwininyumba ngati amakhulupirira ziphunzitso za Mose kukhala zaphindu lerolino. Ngati kuli koyenera kukambirana za Mesiya, choyamba mungaŵerenge Deuteronomo 18:15, imene imati: “Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye.” Funsani mwininyumba za amene Mose anali kunena pamene anati mneneri wonga iye.
5 Ayuda Osapembedza Amaona Zinthu Mosiyana: Si onse amene amati ndi Ayuda amene amakhulupirira ziphunzitso za Chiyuda. Ayuda ambiri ndi achikunja m’malingaliro awo. Amafuna kwambiri kukhala ndi chizindikiro chawo chachiyuda, chokhala ndi chikhalidwe, miyambo ndi maphunziro akeake, m’malo moloŵa chipembedzo cha Chiyuda. Ayuda ena osapembedza amakhulupirira kuti Mulungu ali wosadziŵika—oŵerengeka chabe ndiwo amakana Mulungu. Poyamba, sitingachite zochuluka mwa kugwira mawu kwambiri m’Malemba Achihebri. Kungakhale kopindulitsa kwambiri kuyamba makambiranowo monga mmene mungayambire ndi munthu wina aliyense amene ali wosapembedza. Mwachitsanzo, mungafotokoze mmene Baibulo lilili lothandiza m’nthaŵi yathu ino.
6 Pochitira umboni kwa Myuda, munganene kuti:
◼ “Ambirife tinataya okondedwa athu mu imfa. Kodi muganiza kuti chimatichitikira n’chiyani pamene timwalira?” Yembekezani yankho. Ndiyeno m’sonyezeni mwininyumba bolosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Ndiyeno tsegulani patsamba 31 ndime 2 ndipo m’sonyezeni kuti mogwirizana ndi Malemba, akufa adzaukitsidwa m’dziko lapansi la paradaiso. Ndiyeno gaŵirani boloshali pachopereka chanthaŵi zonse. Pokonzekera ulendo wobwereza, mungatchule kuti kholo lakale Yobu analinso ndi chiyembekezo cha chiukiriro. Gwiritsani ntchito malemba operekedwa kumapeto kwa ndime 1, ndipo nenani kuti mudzabweranso kudzakambirana zimenezi.
7 Mabuku a Mateyu, Marko, Luka, Yohane ndi Machitidwe ali ndi nkhani za Ayuda amene anamvetsera choonadi ndi kuchilabadira. Yehova wasiyabe njira ya kumoyo wosatha ili yotsegula. Ayuda oona mtima ambiri angaphunzirenso za Yehova, Mulungu woona, kuti nawonso akapeze moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu.—Mika 4:1-4.