Kulalikira Kumatisiyanitsa ndi Ena
1 Anthu ambiri amafunsa kuti, “Kodi n’chiyani chimapangitsa chipembedzo cha Mboni za Yehova kusiyana ndi zipembedzo zina?” Kodi inuyo mungayankhe bwanji? Mungafotokoze zina mwa zikhulupiriro zathu za m’Baibulo. Koma kodi munayamba mwalingalirapo zofotokozanso mmene utumiki wathu umatisiyanitsira ndi zipembedzo zina?—Mat. 24:14; 28:19, 20.
2 Lerolino, anthu opembedza ochepa okha ndiwo amasonkhezeredwa kuuza ena zikhulupiriro zawo. Amaganiza kuti ndi kokwanira kumvera malamulo a Kaisara, kukhala ndi makhalidwe abwino, kapena kuchitira ena zabwino. Komabe, saganiza kuti akuyenera kuthandiza ena kuphunzira zimene Baibulo limanena pankhani yopeza chipulumutso. Kodi timasiyana nawo bwanji?
3 Utumiki wathu wachangu umasiyana kwambiri ndi zochita za zipembedzo zina. Kwa zaka zoposa 100, Mboni zamakono, motsatira Akristu oyambirira, zakhala zikulalikira uthenga wabwino mwakhama kufikira kumalekezero a dziko lapansi. Cholinga chathu pochita zimenezi ndicho kuthandiza anthu ambiri kuti miyoyo yawo ikhale yogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.—1 Tim. 2:4; 2 Pet. 3:9.
4 Kodi Mbiri Yanu ndi Yotani? Kodi mumadziŵika monga mlaliki wa Mawu a Mulungu wachangu? (Mac. 17:2, 3; 18:25) Chifukwa cha ntchito yanu yolalikira, kodi anansi anu amasiyanitsa mosavuta chipembedzo chawo ndi chanu? Kodi mumadziŵika monga munthu amene amakhala chire kuti auze ena za chiyembekezo chake? Kodi muli ndi chizoloŵezi chopita mu utumiki? Kumbukirani kuti timadzisiyanitsa osati ndi dzina lathu lokha komanso mwa kuchita zimene dzinalo limanena—kuchitira umboni za Yehova.—Yes. 43:10.
5 Kukonda Mulungu ndi anansi athu kumatisonkhezera kuchita ntchito yolalikira. (Mat. 22:37-39) Ndicho chifukwa chake, mofanana ndi Yesu ndi atumwi, tikufuna kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kuuza ena uthenga wa Ufumu. Tiyenitu tipitirize kulalikira uthenga wabwino mwachangu kwa amene ali ofuna kumvetsera. Kuchita zimenezi kudzathandiza anthu oona mtima “kuzindikira pakati pa . . . iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.”—Mal. 3:18.