Kodi Ndani Angavomere Kuphunzira Baibulo?
1 Mneneri Amosi analengeza kuti mu Israyeli mudzakhala njala, “si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mawu a Yehova.” (Amosi 8:11) Kaamba ka ubwino wa anthu amene ali ndi njala komanso ludzu lauzimu, gulu la Yehova likugaŵira mabuku ofotokoza za Baibulo ambiri kwabasi padziko lonse.
2 Tikunena pano, tasindikiza mabuku a Chidziŵitso okwanira 70 miliyoni ndiponso mabulosha a Mulungu Amafunanji 91 miliyoni. Pophunzitsa choonadi, timayamikira kuti zofalitsa zimenezi sizivuta kumva ndipo n’zogwira mtima. Komabe, anthu ambirimbiri amene analandira zofalitsa zathu sanayambe aphunzira nafe Baibulo. Kodi tingachitepo chiyani?
3 Buku Lililonse Limene Tagaŵira Titha Kuyambitsa Nalo Phunziro! Talingalirani za chokumana nacho cha wofalitsa wina amene paulendo wake woyamba panyumba ya mayi wina anamupempha kuphunzira naye. Nthaŵi yomweyo mayiyo analola. Kenako mayiyo anadzamuuza kuti, “Ndinu munthu woyamba kundipempha kuphunzira nane Baibulo.” M’gawo lanu, ndi anthu angati amene ali nawo kale mabuku athu amene anganene zofananazi? Buku lililonse limene tagaŵira limapereka mpata wopanga ulendo wobwereza ndi wa phunziro la Baibulo lapanyumba.
4 Popeza timakumana ndi anthu amene ali nazo kale zofalitsa zathu, m’motani mmene tingadzutsire chidwi chawo cha kuphunzira zimene zili m’mabuku athuwo? Mboni ina mwachindunji inapempha mwininyumba ngati anali ndi funso lina lililonse la m’Baibulo, n’kuyankhidwa kuti, “Ndilibe.” Mlongoyo sanaimire pomwepo, kenaka anati, “Ndithudi muli nawo.” Mkaziyo anali nawodi mafunso, ndipo anayamba kuphunzira. Bwanji osafunsa mwininyumba ngati angafune kuphunzira zimene Baibulo limanena pafunso kapena nkhani imene imam’detsa nkhaŵa? Khalani okonzeka kufunsa funso lochititsa chidwi ngati iye akuti alibe lililonse. Kukambirana koteroko kudzatsegula njira yophunzira ziphunzitso zikuluzikulu za choonadi cha Baibulo mokhazikika.
5 Kuchititsa maphunziro a Baibulo ndi mbali yofunika kwambiri ya utumiki wathu. Popeza sitidziŵa kuti angavomere kuphunzira n’ndani, musachedwe kufunsa aliyense yemwe mungakumane naye. Muuzeni Yehova nkhaniyo m’pemphero, ndipo chitani zinthu mogwirizana ndi mapemphero anuwo. Mosapita nthaŵi mudzapeza kuti amene mwam’pempha kuphunzira naye walola!—1 Yoh. 5:14, 15.