Maphunziro a Baibulo Enanso Akufunika
1 Yehova Mulungu akudalitsa gulu lake la padziko lapansi ndi chiwonjezeko chomapitiriza. Chaka chatha chautumiki, ophunzira atsopano 375,923 anabatizidwa padziko lonse—oposa 1,000 tsiku lililonse, kapena pafupifupi 43 ola lililonse! Kumadera osiyanasiyana a dziko, ntchito ya Ufumu ikufutukuka ndipo anthu akuwonjezeka modabwitsa, ngakhale kuti abale athu anakumana ndi mavuto pazaka makumi ambiri. Nzosangalatsa kuŵerenga za mmene ntchito yofalitsa uthenga wabwino ikupitira patsogolo!
2 M’gawo la nthambi ya Malaŵi chaka chatha chautumiki, ifenso tinaona kuwonjezeka kwa avareji ya ofalitsa onse ndi apainiya othandiza, maola owonongedwa mu ulaliki, ndi ziŵerengero za timabuku, mabrosha, ndi magazini ogaŵiridwa. Chiŵerengero cha obatizidwa chinawonjezekanso ndipo chiŵerengero cha opezeka pa Chikumbutso chinali chapamwamba koposa ndi kale lonse. Nanga bwanji za maulendo obwereza ndi ntchito ya maphunziro a Baibulo? Ngakhale kuti ziŵerengero zinaonjezeka, ziŵerengero za maulendo obwereza ndi za maphunziro a Baibulo zili pansi penipeni pa avareji. Komanso, mbali zimenezi za utumiki nzofunika kwambiri pantchito yopanga ophunzira. Kodi aliyense wa ife angatani pofuna kuletsa kutsika kwa maulendo obwereza ndi maphunziro a Baibulo?
3 Limbitsani Chikhumbo Chochititsa Phunziro: Ife enife tifunikira kusumika maganizo pa kukhala kwathu olimba ndi okangalika mwauzimu. Otsatira oona a Kristu ali “achangu pa ntchito zokoma.” (Tito 2:14) Pamene tipenda utumiki wathu, kodi tinganene kuti tikufunitsitsa kubwerera kwa amene tinagaŵira mabuku m’munda? Kodi tikufunitsitsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo kwa onse osonyeza chidwi? (Aroma 12:11) Kapena kodi tifunikira kukhala ndi chikhumbo chokulirapo kuti tipange maulendo obwereza ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba?
4 Kuŵerenga Baibulo kwaumwini, kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse, ndi kuŵerenga zofalitsa kudzatithandiza kukhala amoyo mwauzimu ndi amphamvu mwa mzimu wa Mulungu. (Aef. 3:16-19) Zimenezi zidzalimbitsa chikhulupiriro chathu ndi chidaliro mwa Yehova ndi chikondi chathu pa anthu anzathu. Zidzatisonkhezera kuphunzitsa wina wake choonadi, motero kuchititsa utumiki wathu kukhala wosangalatsa, wobala zipatso, ndi wotsitsimula. Inde, tizifuna maphunziro a Baibulo enanso!
5 Phunzirani ndi Banja Choyamba: Makolo achikristu amene ali ndi ana panyumba ayenera kusamalitsa programu yawo ya phunziro la Baibulo la banja lanthaŵi zonse. (Deut. 31:12; Sal. 148:12, 13; Miy. 22:6) Zingakhale zothandiza ngati makolo aphunzira ndi ana awo brosha la Mulungu Amafunanji ndiyeno buku la Chidziŵitso kuwakonzekeretsa kuti adzayenerere kukhala ofalitsa osabatizidwa ndiponso kudzipatulira ndi kubatizidwa. Inde, angapende nawo nkhani zinanso, malinga ndi zosoŵa zomwe zilipo ndi msinkhu wa ana. Kholo lomwe likuphunzira ndi mwana wosabatizidwa lingaŵerengere phunziro, nthaŵi, ndi maulendo obwereza, monga momwe ikufotokozera Mbali ya Mafunso mu Utumiki Wathu Waufumu wa April 1987.
6 Wongolerani Kalinganizidwe Kanu ka Zinthu: Tikaona chiŵerengero cha magazini, mabrosha, ndi mabuku ogaŵiridwa, nzosakayikitsa kuti mbewu zochuluka kwambiri zikufesedwa. Mbewu zimenezi za choonadi zimene zafesedwa zili ndi mphamvu yaikulu yobala ophunzira atsopano. Koma kodi mlimi kapena mwini dimba angakhutiredi ngati amangofesa mbewu ndiyeno, atawononga khama lake lonse, osapeza nthaŵi yotuta? Kutalitali. Momwemonso, utumiki wa maulendo obwereza ngwofunika.
7 Kodi inu nthaŵi zonse mumapatula nthaŵi yopanga maulendo obwereza? Bwererani mwamsanga kwa onse omwe anasonyeza chidwi. Pangani maulendo obwereza ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. Kodi mumakhala ndi pepala labwino, lokhala ndi chidziŵitso chatsopano lolembapo maulendo anu obwereza? Kuwonjezera pa dzina ndi keyala ya mwini nyumba, tsimikizani kulemba deti la ulendo woyamba, zilizonse zomwe munagaŵira, mawu achidule ofotokoza zomwe munakambitsirana, ndi mfundo yomwe mungafutukule paulendo wotsatira. Siyani malo osalembapo kanthu papepala lanulo owonjezapo chidziŵitso chinanso paulendo uliwonse wobwereza.
8 Pendani Mmene Mungapangire Ulendo Wobwereza: Kodi ndi mfundo zina ziti zomwe muyenera kukumbukira popanga ulendo wobwereza kwa munthu amene anachita chidwi? (1) Khalani wansangala, waubwenzi, wolimbikitsa, ndi womasuka. (2) Kambitsiranani nkhani kapena mafunso omwe iyeyo achita nawo chidwi. (3) Makambitsirano anu akhale osavuta, osangalatsa, ndi a m’Malemba. (4) Paulendo uliwonse, yesetsani kuphunzitsa mwini nyumba kanthu kamene iye adzaona kuti nkaphindu kwa iye. (5) Kulitsani chidwi mwa iye m’nkhani imene mudzakambitsirana ulendo wotsatira. (6) Musakhalitse. (7) Musafunse mwini nyumba mafunso omchititsa manyazi kapena ompanikiza. (8) Gwiritsirani ntchito kuzindikira kuti musamatsutse malingaliro olakwa kapena zizoloŵezi zoipa za mwini nyumba iye asanayambe kuyamikira zinthu zauzimu.—Onani mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa March 1997 kuti muthandizikenso ponena za mmene mungakhozere kupanga maulendo obwereza ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
9 Fufuzani Mpata Uliwonse: Mumpingo wina, zinatheka kupeza maina ndi manambala a nyumba za anthu onse okhala m’mdadada wotetezedwa kwambiri. Analembera kalata kwa aliyense wokhala pamenepo, ndipo anaikamo matrakiti aŵiri. Kumapeto kwa kalata, anapempha kuphunzira nawo Baibulo panyumba naphatikizapo nambala yawo ya telefoni kuti wolandira kalatayo akayankhe. Patapita masiku angapo, mnyamata wina anaimba foni napempha kuphunzira. Tsiku lotsatira ulendo wobwereza unapangidwa, ndipo anakhazikitsa phunziro m’buku la Chidziŵitso. Usiku womwewo iye anakapezeka pa Phunziro la Buku la Mpingo, ndipo anapitiriza kupezeka pamisonkhano yonse. Mwamsanga ndithu, anayamba kuŵerenga Baibulo mokhazikika masiku onse ndipo anapita patsogolo kosaleka kulinga ku ubatizo.
10 Kagulu ka ofalitsa ena kanalinganiza kukayenda maulendo obwereza limodzi pagalimoto. Pamene mlongo wina anapanga ulendo kwa mmodzi wa anthu amene anayenera kuwaona, sanapeze munthu yemwe anali kufuna panyumba, koma mtsikana wina anatsegula chitseko, nati: “Ndimakuyembekezerani.” Mwini nyumba analandira buku la Chidziŵitso kwa mnansi. Pamene alongo ankafika pakhomolo, anali ataŵerenga kale buku lonse kaŵiri ndipo anachita chidwi ndi chidziŵitso chake. Anati sanadabwe kuona Mbonizo zikufika kwa iye tsikulo chifukwa anali kupemphera kuti iwo afike kudzaphunzira naye Baibulo. Phunziro linayambika, iye anayamba kupezeka pamisonkhano ya mpingo, ndipo anapita patsogolo mofulumira.
11 Mlongo wina, amene wakhala wobatizidwa kwa zaka pafupifupi 25, posachedwa anapatsa amayi ake buku la Chidziŵitso. Amayi akewo, membala wa tchalitchi, anayamba kuŵerenga bukulo. Atamaliza machaputala aŵiri, anaimbira foni mwana wawoyo, ndipo zinamdabwitsa pamene iwo anati: “Ndikufuna kukhala wa Mboni za Yehova!” Amayiwo anayamba kuphunzira ndipo tsopano ndi obatizidwa.
12 Yesani Malingaliro Aŵa: Kodi munayesapo njira yachindunji yoyambitsira maphunziro? Mungangonena kuti: “Ngati mukufuna kukhala ndi phunziro la Baibulo laulere la panyumba, ndingakusonyezeni pamphindi zingapo chabe mmene timachitira. Ngati lidzakusangalatsani, mukhoza kupitiriza.” Mukanena choncho, anthu ambiri samazengereza kuvomereza ndi kuona mmene phunziro la Baibulo limachitidwira.
13 Kuchiyambi kwa phunziro, sonyezani wophunzirayo mmene azikonzekerera pasadakhale mwa kuŵerenga malemba osonyezedwa ndi kuchonga mawu ofunika kwambiri a mayankho a mafunso osindikiza. Sumikani maganizo kokha pa mfundo zazikulu. Ngakhale kuti tingafunikire kukhala okhoza kusintha pamaphunziro angapo oyambirira, phunziro la Baibulo lifunika kuchitidwa mokhazikika. Ganizirani za mmene mudzaloŵetserapo pemphero monga mbali yofunika paphunziro ndi mmene mwamalemba mudzakonzekeretsera wophunzirayo pa chitsutso. Chitani zomwe mungathe kuti phunzirolo likhale laumoyo.
14 Inde, si ophunzira Baibulo onse amene amapita patsogolo pamlingo wofanana. Ena sakonda kwambiri zauzimu monga amachitira ena ndiponso ena safulumira kugwira zinthu zimene akuphunzira. Ena ali otanganidwa kwambiri ndipo sakhoza kukhala ndi nthaŵi yofunikira kuti amalize mutu wonse mlungu uliwonse. Chotero, kwa ena pangafunikire kuchita phunzirolo kangapo kuti amalize mitu ina ndi miyezi inanso kuti amalize buku lonse. Nthaŵi zina tingayambe kuphunzira brosha la Mulungu Amafunanji ndiyeno nkupitiriza m’buku la Chidziŵitso; nthaŵi zina, titatsiriza buku la Chidziŵitso, tingaone kuti ndi bwino kuphunziranso brosha lakuti Mulungu Amafunanji? Zimenezi, limodzi ndi kupezeka pamisonkhano ya mpingo, zidzathandiza wophunzira aliyense kukhala ndi maziko olimba m’choonadi.
15 Koposa zonse, pempherani kuti mukhale ndi phunziro la Baibulo! (1 Yoh. 3:22) China cha zinthu zofupa kwambiri kwa Mkristu ndicho kugwiritsidwa ntchito ndi Yehova kuthandiza wina wake kukhala wophunzira wa Yesu Kristu. (Mac. 20:35; 1 Akor. 3:6-9; 1 Ates. 2:8) Ino ndiyo nthaŵi yokangalika kwambiri pantchito ya maphunziro a Baibulo, tikumakhala ndi chidaliro chonse chakuti Yehova adzadalitsadi khama lathu poyambitsa maphunziro enanso!
[Mawu Otsindika patsamba 3]
Kodi mukupemphera kuti muyambitse phunziro la Baibulo latsopano?