Maulendo Obwereza Amathandiza Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo
1. N’chifukwa chiyani kupanga maulendo obwereza n’kofunika kwambiri?
1 Yesu sanalamule otsatira ake kuti azingolalikira komanso kuti ‘aziphunzitsa.’ (Mat. 28:19, 20) Mlaliki amalalikira, koma mphunzitsi amachita zambiri. Amalangiza, kufotokoza, ndiponso kupereka umboni wa zimene wafotokoza. Kupanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi n’cholinga choyamba kuphunzira nawo Baibulo ndi njira imodzi imene timaphunzitsira anthu ena.
2. Kodi tiyenera kubwerera kwa ndani?
2 Kodi tiyenera kupanga maulendo obwereza kwa ndani? Onetsetsani kuti mwabwerera kwa anthu onse amene analandira mabuku kapena amene anachita chidwi ndi uthenga wabwino, ngakhale chitakhala chochepa. Mukapeza munthu wachidwi polalikira malo a anthu ambiri, tengani adiresi kapena telefoni ya munthuyo kuti mudzapitirize kukulitsa chidwi chakecho. Tsimikizani mtima kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Pitirizani kufunafuna anthu amene angavomere kuphunzira Baibulo, ndipo mudzawapezadi.—Mat. 10:11.
3, 4. Kodi m’pofunika chiyani kuti maulendo obwereza akhale ogwira mtima?
3 Chitani Nawo Chidwi: Kukonzekera ulendo wobwereza wogwira mtima kumayambira paulendo woyamba. Olalikira amene zimawayendera bwino amaona zimene zimasangalatsa mwininyumba, ndipo amagwiritsa ntchito zimenezo monga poyambira kukambirana zina. Ena amaona kuti zimathandiza kufunsa funso pamapeto pokambirana kuti mwininyumba ayembekezere mwachidwi ulendo winawo. Kuchitadi chidwi ndi anthu kumatithandiza kuti tiziwaganizirabe ngakhale tikasiyana nawo, ndipo zimatilimbikitsa kubwererakonso mofulumira. Ngati n’kotheka pitaniko akadali ndi chidwi, mwina patapita tsiku limodzi kapena aŵiri.
4 Paulendo wobwereza, yesani kupitiriza zimene munakambirana paulendo woyamba. Khalani ndi cholinga chakuti paulendo uliwonse muzikambirana mfundo yolimbikitsa ya m’Malemba yosachepera imodzi, ndipo khalani wofunitsitsa kumvetsera. M’dziŵeni bwino mwininyumbayo. Ndiyeno paulendo wobwereza, kambiranani naye mfundo za m’Mawu a Mulungu zokhudza kwambiri zimene zimam’detsa nkhaŵa.
5. Kodi ndi njira yosavuta iti imene ingagwire ntchito poyambitsa maphunziro a Baibulo?
5 Khalani Wofunitsitsa Kuyambitsa Phunziro la Baibulo: Pangani maulendo obwereza ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Muuzeni kuti mukufuna kumuuza mfundo ina yosangalatsa, ndiyeno pitani m’buku la Chidziŵitso kapena m’bulosha la Mulungu Amafunanji pandime imene mukuganiza kuti imusangalatsa. Ŵerengani ndimeyo, funsani funso, ndi kukambirana lemba limodzi kapena aŵiri a pa ndimeyo. Mungachite zimenezi mutangoima pa khomo pomwepo kwa mphindi zisanu kapena khumi. Malizani ndi kufunsa funso lotsatira ndiponso kukonza zodzapitiriza kukambiranako nthaŵi ina.
6. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timazindikira kufunika kopanga maulendo obwereza?
6 Kukulitsa chidwi chilichonse chimene tapeza ndi mbali yofunika ya utumiki wathu. Choncho, pa ndandanda yanu ya mlungu uliwonse patulani nthaŵi yopanga maulendo obwereza. Kuchita zimenezi kudzathandiza kuti utumiki wanu ukhale wogwira mtima ndipo mudzapeza chimwemwe chenicheni.