Thandizani Anthu Amaganizo Abwino
1. Kodi Yehova akusonkhanitsa ndani masiku athu ano?
1 Munthu aliyense ali ndi khalidwe linalake lomwe linazika mizu mu mtima wake wophiphiritsa. (Mat. 12:35) Baibulo limatchula za munthu amene ‘mumtima mwake muli nkhondo.’ (Sal. 55:21) Anthu ena ‘ngaukali.’ (Miy. 29:22) Koma palinso ena “ofuna moyo wosatha.” (Mac. 13:48, NW) Masiku athu ano, Yehova akusonkhanitsa anthu amaganizo abwino ameneŵa. (Hag. 2:7) Kodi tingawathandize motani kuti akhale olambira Yehova?
2. Kodi pamafunikanji kuti tikwaniritse ntchito yathu yopanga ophunzira?
2 Yesetsani Kubwererako: Kuti tikwaniritse ntchito yathu yopanga ophunzira, tifunika kukhala ndi maganizo abwino pankhani yopanga maulendo obwereza. (Mat. 28:19, 20) Kodi timabwererako mwamsanga kwa anthu achidwi? Kodi timapitanso kwa anthu onse amene alandira mabuku kapena amene achita chidwi ndi uthenga wabwino? Kodi timachita khama kuwathandiza kuti akule mwauzimu? Poti nkhaniyi ikukhudza moyo, tiyenera kuyesetsa kukulitsa chidwi cha anthu onse amene tapeza.
3. Kodi tiyenera kuchitanji tikatha kukambirana ndi munthu mu utumiki?
3 Musanaiŵale zomwe mwakambirana ndi munthu wachidwi, pezani nthaŵi yolemba dzina ndi malo omwe akukhala. Lembani nkhani yomwe mwakambirana, malemba onse omwe mwaŵerenga, ndi buku lomwe mwam’siyira. Kenako, kumbukirani kubwererako mwamsanga.
4. Kodi tingapange bwanji maulendo obwereza ogwira mtima?
4 Kupanga Ulendo Wobwereza: Popanga ulendo wobwereza, ndi bwino kukhala waubwenzi ndi wansangala ndiponso kusonyeza kuti muli ndi chidwi ndi mwininyumbayo. Feŵetsani nkhaniyo ndipo ikhale ya m’Malemba. Konzekerani kukambirana nkhani yosangalatsa ya m’Baibulo, ndipo pomaliza kukambiranako, perekani funso lomwe mudzayankhe paulendo wotsatira. Si bwino kumangotsutsa maganizo alionse osagwirizana ndi Malemba amene mwininyumbayo angafotokoze. Yesetsani kukambirana nkhani zimene nonse mukuzidziŵa.—Akol. 4:6.
5. Kodi mpainiya wina anachita khama lotani, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
5 Pamafunika khama kuti tipange maulendo obwereza, koma zotsatira zake zimakhala zosangalatsa. Mpainiya wina ku Japan anakonza zoti azipanga maulendo obwereza ambiri mwezi uliwonse. Anayamba kulemba anthu onse amene wakumana nawo pa ntchito ya ulaliki wa kunyumba ndi nyumba, ndiyeno anawapitiranso pasanathe masiku asanu ndi aŵiri. Ankakonzekera bwino zoti akanene ndipo ankachita utumiki wake akuudalira kwambiri uthenga womwe anali nawo. Paulendo wina wobwereza, iye anayamba kuphunzira ndi munthu wina yemwe anati: “Ndakhala ndikukana kuti anthu inu mubwere pano. Aka n’koyamba kukumvetserani.” Khama ndiponso chikondi cha mpainiyayo chinapindula. Pamapeto pa mweziwo anapereka lipoti la maphunziro a Baibulo khumi.
6. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita khama kupanga maulendo obwereza?
6 Miyoyo ya anthu ikusinthasintha. (1 Akor. 7:31) Nthaŵi zambiri pamafunika kuyenda maulendo angapo kuti tim’pezenso munthu wachidwi panyumba. Mwa kuyesetsa kupanga maulendo obwereza, tingathandize anthu amaganizo abwino kubwera panjira ya ku moyo wosatha.—Mat. 7:13, 14.