Kukulitsa Chikondwerero pa Maulendo Obwereza
1 Moyenerera, utumiki wayerekezeredwa ndi ulimi, ndipo kupanga maulendo obwereza kwayerekezeredwa ndi kupalira ndi kuthirira. (Mat. 13:23; Luka 10:2; 2 Akor. 9:10) Monga “antchito anzake a Mulungu,” tili ndi thayo la kuthandiza mbewu iliyonse yomera chatsopano kukula ndi kukhala yobala zipatso. (1 Akor. 3:6, 9) Kodi njira yabwino koposa yochitira zimenezi ndi iti?
2 Khalani ofulumira kupanga maulendo obwereza kwa onse amene asonyeza chikondwerero. Pendani zolembedwa zanu za kunyumba ndi nyumba, ndipo sankhani amene mudzachezera ndi zimene mudzakambitsirana naye. Kaŵirikaŵiri mutu wanu wokambitsirana udzadalira pa zimene munakambitsirana paulendo woyamba. Khalani wokhoza kusintha, mukumakumbukira malingaliro ena a Malemba amene mungatchule. Ndi bwino kugwiritsira ntchito Baibulo nthaŵi zonse, pozindikira mphamvu yake ya kufika pa mtima.—Aheb. 4:12.
3 Ngati munasiyako brosha lakuti “Kodi Mulungu Amatisamaliradi?,” mungayambe mwa kunena zonga izi:
◼ “Anthu ambiri oona mtima amakhulupirira kuti Mulungu adzawononga dziko lapansi, pamene ena amawopa kuti munthu mwiniyo ndiye adzachita zimenezo. Kodi muganiza bwanji? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limatiuza kuti mmalo mowononga dziko lapansi, Mulungu adzaliyeretsa kuchotsapo zosalungama, kulipanga kukhala malo a mtendere ndi chisungiko.” Sumikani maganizo patsamba 22, ndipo ŵerengani Miyambo 2:21, 22, imene yagwidwa mawu pamenepo. Ngati asonyeza chikondwerero, fotokozani makonzedwe a phunziro la Baibulo lapanyumba kapena gaŵirani magazini atsopano, ndi kupanga makonzedwe a kubweranso kudzakambitsirana zambiri ponena za lonjezo la Mulungu la dziko latsopano.
4 Ngati munagaŵira brosha lakuti “Tawonani!,” munganene kuti:
◼ “Paulendo wanga wapapitapo, tinaŵerenga m’Baibulo ponena za lonjezo la Mulungu la kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso, wonga amene wasonyezedwa pachithunzithunzi cha pachikuto cha brosha limene ndinakusiyirani. Ife tingapeze madalitso ameneŵa mwa kuphunzira zambiri ponena za chifuniro cha Mulungu ndi mmene chimatiyambukirira.” Ŵerengani Yohane 17:3, ndiyeno tsegulani pa ndime 52 ndi 53 patsamba 27. Fotokozani mwachidule chifukwa chake kuli kofunika kupeza chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu.
5 Pobwerera kumene munagaŵira brosha lakuti “Chifuno cha Moyo” kwa munthu wopembedza, kungakhale koyenera kwa inu kunena kuti:
◼ “Mosakayikira konse inu nthaŵi zambiri mwabwereza Pemphero la Ambuye. Kodi mumaganiza chiyani pamene mupempha kuti Ufumu wa Mulungu udze?” Pambuyo poti mwininyumba wayankha, pitani pa ndime 8 ndi 9 patsamba 26, ndiyeno ŵerengani Danieli 2:44. Mwinamwake mungapitirize kukambitsiranako mwa kufotokoza kuti kudza kwa Ufumu wa Mulungu kudzatanthauza mapeto a kuipa ndi kuvutika. Tchulani kuti ngati tili olungama pamaso pa Mulungu, tingapeze moyo wosatha m’Paradaiso pa dziko lapansili.
6 Kumbukirani kuti ulendo wobwereza ungapangidwe kwa aliyense amene anali wofunitsitsa kumva, kaya munagaŵira buku kapena ayi. Yesani kupatula nthaŵi mlungu uliwonse yopangira maulendo obwereza. Yehova adzadalitsa kuyesayesa kwanu kwa khama kwa kukulitsa chikondwerero chimene mupeza. Chibaletu zipatso ku chitamando chake.—Yoh. 15:8.