Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/95 tsamba 4
  • Pangani Maulendo Obwereza pa Mabrosha Onse Amene Munagaŵira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pangani Maulendo Obwereza pa Mabrosha Onse Amene Munagaŵira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Lengezani Uthenga Wabwino wa Ufumu ndi Mabrosha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Gwiritsirani Ntchito Mabrosha Osiyanasiyana Mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 7/95 tsamba 4

Pangani Maulendo Obwereza pa Mabrosha Onse Amene Munagaŵira

1 Mtumwi Paulo anayamikira Afilipi chifukwa chakuti ‘anatsitsimutsanso kulingirira mtima za kwa iye.’ (Afil. 4:10) Ngati tigwiritsira ntchito chitsanzo chawo monga choonerapo cha utumiki wakumunda, ‘tidzatsitsimutsa kulingilira mtima’ za awo amene timalalikirako ndipo tidzasonkhezereka kupanga maulendo obwereza.

2 Ngati munagaŵira brosha lakuti “Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso,” munganene zonga izi:

◼ “Ndinali kulingalira pa zimene tinakambitsirana tsiku lija, ndiyeno ndakumbukira malemba aŵiri amene ndifuna kukambitsirana nanu. Ndiyesa mukukumbukira kuti tinakambitsirana zakuti Mulungu adzatenga ulamuliro wa dziko lapansi. M’Baibulo, Yehova Mulungu walonjeza kuti zimenezi zidzachitika. [Ŵerengani Danieli 2:44.] Kodi mukukhulupirira kuti zimenezi zidzachitikadi? [Yembekezani yankho.] Tamverani zimene Mulungu akunena za mphamvu yake ya kukwaniritsa malonjezo ameneŵa. [Ŵerengani Yesaya 55:11.] Kodi zimenezo siziyenera kutisonkhezera kuika chidaliro chathu mu Ufumu wa Mulungu? Koma kodi ndiliti pamene Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake?” Nenani kuti mudzayankha funso limenelo mukadzabweranso.

3 Mwina mungagwiritsire ntchito kafikidwe aka paulendo wobwereza kwa munthu amene anatenga brosha lakuti “Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira”:

◼ “Ndayesa ndithu kuti ndibwerenso, kaamba ka nkhani yathu ija ya kutaya munthu mu imfa.” Sonyezani chithunzithunzi patsamba 30 pamene munena kuti: “Kodi mukukumbukira chochitika chosangalatsa ichi cha anthu amene akuukitsidwa ndi kukhalanso pamodzi ndi okondedwa awo? Paja ndinakusiyani ndi funso lonena za kumene zimenezi zidzachitikira, kumwamba kapena pa dziko lapansi. Mwinamwake munapeza yankho la Baibulo patsamba 26 m’brosha limeneli.” Kambitsiranani mfundo zazikulu m’ndime yachitatu mpaka yachisanu, ndipo ŵerengani Yohane 5:21, 28, 29. Malinga ndi nthaŵi imene muli nayo, ŵerengani iliyonse ya malemba enawo patsamba limenelo.

4 Kodi munayambitsa phunziro m’brosha lakuti “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”? Paulendo wobwereza, mungachite izi:

◼ Pitaninso patsamba 30, ndi kusonyeza funso lakuti: “Kodi Baibulo lili lapadera m’njira zotani?” Pitani pamasamba 3 ndi 4, ndi kukambitsirana ndime 1-4 limodzinso ndi chithunzithunzi pachikuto cha broshalo. Ŵerengani lemba limodzi kapena aŵiri m’mawu amtsinde pandime 4. Longosolani kuti Baibulo ndilo buku lokha limene limapereka chiyembekezo chodabwitsa choterocho. Panganani za ulendo wotsatira. Pambuyo pa ulendo wachitatu, ngati zikuoneka kuti phunziro lidzapitiriza, mungayambe kuchitira lipoti phunziro latsopanolo!

5 Mungapitirize kukambitsirana kwa brosha lakuti “Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha” mwa njira iyi:

◼ “Pamene ndinali pano, ndinakusonyezani dzina la Mulungu m’Baibulo. Kudziŵa ndi kutchula dzina la Yehova nkofunika kwambiri pa kulambira kwathu.” Tsegulani patsamba 31, fotokozani mfundo zazikulu m’ndime zinayi zomalizira, ndi kuŵerenga Yohane 17:3 ndi Mika 4:5. Fotokozani kuti timapereka programu ya kuphunzira Baibulo imene ingasonyeze mmene dzina la Mulungu lidzayeretsedwera m’njira yoyenera ndi mmene tingapezere madalitso a dziko lapansi la paradaiso.

6 Chotero, tsitsimutsani kulingilira mtima za aja amene mwakambitsirana nawo. Pitirizanibe kumabwererako, ndipo konzekerani zokambitsirana nawo zopindulitsa. Mungakhale aja “amene abaladi zipatso” mwa kupanga ophunzira atsopano.—Mat. 13:23.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena