Asonyezeni Nkhaŵa Yeniyeni Ochita Chidwi Onse Omwe Mwapeza
1 Kulengeza za Ufumu padziko lonse kudzatha posachedwapa, pambuyo pake onse “osamdziŵa Mulungu” adzawonongedwa. (2 Ates. 1:7-9) Chotero, nkhaŵa yeniyeni ya moyo wa ena ikusonkhezera anthu a Yehova kufikira anthu ambiri ndi uthenga wa Ufumu.—Zef. 2:3.
2 Mwezi uliwonse, amatha maola mamiliyoni ambiri pofunafuna aja omwe amafuna kumva “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Yes. 52:7) Atalandira buku limene tikugaŵira, ambiri alandira makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kapena brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Nkhaŵa yeniyeni ya anthu ameneŵa iyenera kutisonkhezera kubwerera kwa onse amene anasonyeza chidwi.—Miy. 3:27.
3 Khalani ndi Zolembapo Zolondola: Mudzachita zambiri mwa kulemba molondola maina a ochita chidwi ndiponso zimene mwagaŵira. Chidziŵitso chonga dzina ndi keyala ya mwini nyumba, tsiku ndi nthaŵi imene munamfikira, mabuku omwe munamgaŵira, ndi mutu wa nkhani imene munakambitsirana zidzakuthandizani kukhala wogwira mtima mutabwererako. Ndiponso, ngati mulemba ndemanga zina zimene mwini nyumba ananena pakukambitsirana kwanu koyamba, mungadzazitchule mogwira mtima pamene mukupitiriza kukambitsiranako paulendo wobwereza.
4 Fulumirani Kubwererako: Kodi ndi angati amene munagaŵira mabuku mwezi wathawu omwe munayesa kukawachezeranso? Kodi papita milungu yambiri popanda kuonananso? Kudera nkhaŵa kwenikweni ubwino wawo wosatha kuyenera kukusonkhezerani kubwererako msanga, pambuyo pa masiku oŵerengeka, pamene mukukumbukirabe makambitsiranowo. Mwa kubwererako msanga kukawonjezera chidwi chawo, mungamtsekereze Satana ‘asanadze kudzachotsa mawu ofesedwa mwa iwo.’—Marko 4:15.
5 Kukonzekera Nkofunika: Kuti mukhale wogwira mtima paulendo wobwereza zimadalira pa kukonzekera bwino. Lingalirani zimene muti mukanene musanapite. Tsamba lakumbuyo la Utumiki Wathu Waufumu wa April 1997 lili ndi maulaliki angapo amene mungagwiritsire ntchito mwachipambano pogaŵira magazini kapena brosha la Mulungu Amafunanji. Chinthu china ndicho kukhala ndi mfundo zina m’maganizo zokakamba mutabwererako. Kodi munganenenji pamene mwabwerera kwa wochita chidwiyo? Nanga mungayambe bwanji phunziro la Baibulo?
6 Pamene mukupitiriza kukambitsirana za chimene chikufunika kuti dzikoli liyere nilikhale malo abwino okhalamo, munganene kuti:
◼ “Paulendo wanga woyamba, tinavomerezana kuti dziko lapansili lisanakhale paradaiso wamtendere, payenera pachitike zamphamvu ndithu. Kodi mukuganiza kuti anthu ali nazo zofunika kuti akwanitse ntchito imeneyo? [Yembekezerani yankho.] Chonde taonani chifukwa chake kuli koyenera kuti Mulungu adzaloŵerere m’zochita za anthu.” Ŵerengani Salmo 37:38. Ndiyeno pitani pa phunziro 5 m’brosha la Mulungu Amafunanji, ndipo gwiritsirani ntchito zigawo zimene mwasankha m’ndime 4-5 kuti musonyeze mmene Mulungu adzakwaniritsira ulosi umenewu. Pitirizani mwa kumpempha kuphunzira naye Baibulo, kugwiritsira ntchito brosha lomwelo.
7Ngati munakambitsirana za Ufumu wa Mulungu paulendo woyamba ndi kugaŵira brosha la “Mulungu Amafunanji,” pamene mubwererako munganene zonga izi:
◼ “Pakucheza kwathu koyamba kuja, tinaona kuti Ufumu wa Mulungu ndilo boma lenileni limene lidzalamulira padziko lonse lapansi. Baibulo limasonyeza kuti Kristu Yesu ndiye adzakhala wolamulira wake. Kodi mukuona mapindu alionse a kukhala ndi boma ndi mtsogoleri wamtundu umenewu?” Yembekezerani yankho. Tsegulani brosha la Mulungu Amafunanji paphunziro 6. Pogwiritsira ntchito mfundo zimene mwasankha m’ndime 6-7 ndi chithunzithunzi patsamba 13, sonyezani zimene Ufumu wa Mulungu udzachitira anthu mtsogolomu. Ŵerengani Danieli 2:44, ndipo ngati nkoyenera, sonyezani buku la Chidziŵitso ndi kumpempha kuphunzira naye Baibulo.
8 Ngati munapeza wina yemwe anavomereza kuti zipembedzo zadziko zaloŵetsa anthu m’mavuto, mutabwererako mungafunse kuti:
◼ “Kodi munayamba mwaganizapo kuti tingadziŵe motani chipembedzo chimene Mulungu amavomereza? [Yembekezerani yankho.] Brosha ili, lakuti, Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? likupereka zizindikiro zodziŵira chipembedzo choona.” Pitani pa phunziro 13, ndipo sonyezani mfundo zisanu zakanyenye m’ndime 3-7. Mungapitirize mwa kunena kuti: “Kuwonjezera pa kupeza chipembedzo choona, tiyenera kudziŵa zimene Mulungu amafuna kwa ife aliyense payekha.” Ŵerengani Yohane 4:23, 24. Muuzeni kuti muli wokonzeka kukambitsirana naye zambiri. Pitani pa phunziro 1 m’broshalo, ndipo sonyezani mmene timaphunzirira.
9 Ngati mukubwerera kukapitiriza kukambitsirana za chimwemwe cha banja, munganene zina zofanana ndi zotsatirazi:
◼ “Pamene tinakumana poyamba, ndinakuuzani chinsinsi cha chimwemwe cha banja, chomwe chili kugwiritsira ntchito uphungu wopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Ponena za kusamalira zosoŵa za banja lamakono, kodi mumakhulupirira kuti Baibulo ndi lachikale kapena ndi lamakono?” Yembekezerani yankho. Mpatseni buku la Chidziŵitso. Pitani pa mutu 2, ndipo ŵerengani mawu ogwidwa m’ndime 13. Mwakugwiritsira ntchito mfundo zili m’ndime 3, pemphani kuphunzira Baibulo ndi banja lonse.
10 Mwa kukhala ndi zolembapo zolondola, kukonzekera bwino, ndi kubwererako msanga kukawonjezera chidwi chawo, tingasonyeze mtundu wa chikondi chamnansi chimene chidzawakopera panjira yachipulumutso.—Mat. 22:39; Agal. 6:10.