Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/97 tsamba 8
  • Dalirani Yehova Kuti Akulitse Zinthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dalirani Yehova Kuti Akulitse Zinthu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Maulaliki Amene Mungagwiritse Ntchito mu Utumiki wa Kumunda
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Kuyambitsa Maphunziro m’Bolosha la Mulungu Amafunanji
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 8/97 tsamba 8

Dalirani Yehova Kuti Akulitse Zinthu

1 “Kwa Nthaŵi Yoyamba Ndinamva Chimwemwe Chachikulu Pamene Ndinathandiza Kukhazikitsa Mpingo Watsopano. Zimenezi Zinatheka Patapita Zaka Zoposa Ziŵiri Za Ntchito Yakhama, Mapemphero Akaŵirikaŵiri Ndi Kudalira Yehova Amene ‘Amakulitsa.’” Analemba Choncho Mpainiya Wina Wachangu Yemwe Anaphunzira Kudalira Yehova Kuti Zinthu Zikule. (1 Akor. 3:5-9) Pamene Tikufunafuna Anthu Okonda Zauzimu, Nafenso Tifunikira Kuti Mulungu Atichirikize Kuti Utumiki Wathu Ubale Zipatso.—Miy. 3:5, 6.

2 Kuti Zinthu Zikule Zimafuna Kulimirira: Mbewu ya choonadi imafuna kulimiriridwa kuti ikule. Tikabwererako patapita tsiku limodzi kapena masiku aŵiri kaŵirikaŵiri pamakhala zotsatirapo zabwino. Khalani wachimwemwe ndi waubwenzi. Mpangitseni munthuyo kukhala womasuka. Musalankhule nokha iyayi. Mloleni iyenso akudziŵeni, ndipo msonyezeni kuti mukukondwera naye monga munthu.

3 Mu July mpaka mu August yense, tikulimbikira kugaŵa mabrosha osiyanasiyana kwa anthu amene tizikumana nawo. Komabe, tifunikiranso kukulitsa chidwi cha anthu omwe tapeza ndi kupita kwa aja amene tinagaŵira mabuku. Timatero mwa kupanga maulendo obwereza ndi kuwapempha anthu kuphunzira nawo Baibulo. (Mat. 28:19, 20) Ndi cholinga chimenecho, tingagwiritsire ntchito brosha la Mulungu Amafunanji kuti tiyambitse maphunziro. Malingaliro anayi otsatirawa angakhale othandiza.

4 Ngati munalankhulapo ndi wina yemwe anali wodera nkhaŵa za mmene zinthu zikuyendera padziko, mungayambenso kukambitsiranako mwa kunena kuti:

◼ “Ndikhulupirira kuti inunso mukudera nkhaŵa ngati ine ndemwe za kuwonongeka kwa khalidwe la anthu. Timamva malipoti osautsa a chiwawa panyumba, chimene chimavulaza ana, makolo, ndi mwamuna kapena mkazi wake. Ndipo anthu ambiri sikumawavuta kunama kapena kuba kuti akhutiritse zikhumbo zawo. Kodi mukuganiza kuti Mulungu ali nazo kanthu mmene anthu amakhalira? [Yembekezerani yankho.] Mulungu anaika malamulo omwe munthu ayenera kumvera, ndipo iwo satilemetsa iyayi.” Ŵerengani 1 Yohane 5:3. Ndiyeno perekani brosha la Mulungu Amafunanji, ndipo tsegulani pa phunziro 10. Ŵerengani ndime yoyamba. Sonyezani mawu a kanyenye kuchiyambi kwa ndime 2-6, ndiye mfunseni mwini nyumbayo kuti ndi machitachita ati amene akuganiza kuti amavulaza anthu kwambiri. Ŵerengani ndime yake ndi kuŵerenga lemba limodzi kapena aŵiri ngati mpata ulipo. Malizani mwa kuŵerenga ndime 7, kenako panganani kuti mudzabwerenso kudzakambitsirana zambiri.

5 Kwa aja amene munakumana nawo omwe amasamala za banja lawo, munganene zonga izi:

◼ “Kodi mukuganiza kuti nkwanzeru kuyembekezera kuti Mlengi angatipatse zipangizo zimene tifuna kuti timangire moyo wabanja wachimwemwe?” Yembekezerani yankho. Sonyezani brosha la Mulungu Amafunanji, pitani pa phunziro 8, ndipo fotokozani kuti lili ndi mapulinsipulo ochokera m’Baibulo kwa munthu aliyense m’banja. Apempheni kuwasonyeza mmene angagwiritsirire ntchito broshalo ndi Baibulo kuti apezemo mapindu aakulu. Tsatirani malangizo amene ali patsamba 2 la broshalo. Panganani kuti mudzabwerereko kukapitiriza phunzirolo, kapena ngati mwalitsiriza, kuti mukayambe phunziro lina limene mwini nyumbayo wasankha m’broshalo.

6 Nayi njira yachindunji imene mungagwiritsire ntchito kuyamba programu yathu ya phunziro la Baibulo. Sonyezani brosha la “Mulungu Amafunanji” ndi kunena kuti:

◼ “Brosha lino lili ndi kosi yonse yolongosola ziphunzitso zoyambirira za Baibulo. Patsamba lililonse, mupezapo mayankho a mafunso amene avutitsa anthu kwa zaka mazana ambiri. Mwachitsanzo, Kodi chifuno cha Mulungu padziko lapansi nchiyani?” Pitani pa phunziro 5, ndipo ŵerengani mafunso ali kuchiyambi kwa phunzirolo. Mfunseni mwini nyumba funso limene lamkondweretsa kwambiri, ndiye ŵerengani ndime yake (zake), ndi kuŵerenga malemba oyenera. Mfotokozereni kuti angapeze mayankho okhutiritsa a mafunso ena mosavuta monga mmene mwapezera linali. Gaŵirani broshalo pachopereka cha K3.60. Pemphani kuti mudzabwerenso kudzakambitsirana funso lina ndi kuliyankha.

7 Mwina mungakonde kuyesa njira yosavuta yoyambira phunziro la Baibulo mwa kunena kuti:

◼ “Kodi mukudziŵa kuti pamphindi zoŵerengeka chabe mungapeze yankho la funso lalikulu m’Baibulo? Mwachitsanzo, . . .” Kenako funsani funso lili kuchiyambi kwa limodzi la maphunziro a m’broshalo, limene mukuganiza kuti lingamchititse chidwi munthuyo. Ponena za malingaliro ena a mafunso amene mungafunse, onani ndime 15 ndi 16 mu Utumiki Wathu Waufumu wa May 1997 zakuti: “Limbani Mtima Kuti Mupange Maulendo Obwereza.”

8 Kuilandira mwachimwemwe ntchito yopanga maulendo obwereza ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo ndiko kukhala “antchito anzake” a Mulungu. (1 Akor. 3:9) Tikamalimbikira kulimirira chidwi cha anthu amene timapeza kenako nkudalira Yehova kuti akulitse zinthu, tidzakhaladi okhutira kuposa mmene tingakhalire pantchito ina iliyonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena