Kuyambitsa Maphunziro m’Bolosha la Mulungu Amafunanji
1 Malipoti ochokera padziko lonse akusonyeza kuti bolosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? ndi chida champhamvu chophunzitsira anthu choonadi. Maphunziro a Baibulo zikwizikwi akuyambidwa mlungu uliwonse m’bolosha limeneli. Kodi mwakhalapo okhoza kuyambitsa ndi kuchititsa phunziro la Baibulo m’bolosha la Mulungu Amafunanji?
2 Pamene kuli kwakuti ambiri savutika kugaŵira boloshali, ena amasoŵa zonena kuti ayambe phunziro. Kodi ndi njira zotani zimene ena aona kuti ndi zothandiza poyambitsa maphunziro a Baibulo mwa kugwiritsa ntchito bolosha la Mulungu Amafunanji? Malingaliro awa angakhale othandiza.
3 Sonyezani Mmene Phunziro Limachitidwira: Paulendo woyamba kapena wobwereza, m’malo mouza mwininyumba za phunziro la Baibulo, tingamsonyeze mmene kosi ya phunziro la Baibuloyo idzachitidwira. Zimenezi zidzawachotsera malingaliro akuti n’zachinsinsi ndi mantha alionse amene eninyumba ambiri amakhala nawo akamva mawu akuti “phunziro.” Titangophunzira mmene tingalisonyezere, tidzaona kuti ndi mawu oyamba pang’ono chabe tingayambe phunziro.
4 Chinsinsi Chake ndi Kukonzekera: Kufunitsitsa kwathu kuyambitsa maphunziro a Baibulo kumagwirizana mwachindunji ndi mmene ifeyo takonzekerera bwino. Kukonzekera pasadakhale kudzatithandiza kusakayikira kugwira nawo ntchito yochititsa maphunziro a Baibulo. Mwa kuyeserera ulaliki wathu nthaŵi zochuluka, tidzatha kukambirana bwino ndi ena, tikumalongosola zinthu mwachibadwa ndiponso m’mawu athuathu. Zimenezi sikuti zidzangothandiza ifeyo kukhala omasuka komanso mwininyumba naye adzamasukanso.
5 Pamene mukuyeserera, ndi bwino kuona nthaŵi imene ulaliki wanu ukutenga kuti mukathe kumuuza mwininyumba nthaŵi imene mudzatenga kuti mumsonyeze phunzirolo. Mbale wina atadzidziŵikitsa amati: “Ndafika pano kuti ndikuonetseni pologalamu yathu ya phunziro la Baibulo yaulere. Kumatenga mphindi ngati zisanu kusonyeza mmene timachitira. Kodi tingacheze kwa mphindi zisanu?” Phunziro 1 la bolosha la Mulungu Amafunanji lingasonyezedwe mphindi pafupifupi zisanu. Zoonadi, ndi malemba ochepa chabe amene angaŵerengedwe m’nthaŵi imeneyi, koma mwa kutsiriza phunziro loyamba m’mphindi zochepa, mwininyumbayo adzakhala ndi phunziro lake loyamba. Ndiyeno muuzeni kuti pamene mudzabweranso kudzaphunzira Phunziro 2, mudzatenga mphindi 15 zokha.
6 Ulaliki uwu wakhala wogwira mtima:
◼ “Ndikufuna ndikusonyezeni mmene timachitira kosi ya phunziro la Baibulo la panyumba yosavuta, komabe yofulumira, pogwiritsa ntchito bolosha ili lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Ambiri aona kuti m’mphindi zochepa chabe ngati 15 pa mlungu kwa milungu 16, angapeze mayankho okhutiritsa a m’Malemba onena za mafunso a m’Baibulo ofunika awa.” Mwachidule msonyezeni mpambo wa zam’katimu. Pitani pa Phunziro 1 ndi kunena kuti: “Ngati mungatipatseko mphindi zisanu, tingakonde kukusonyezani mmene zimenezi zimachitikira. Phunziro 1 lili ndi mutu wakuti ‘Mmene Mungadziŵire Zimene Mulungu Amafuna.’” Kenako ŵerengani mafunso atatuwo, ndi kulongosola chimene manambala omwe ali m’mabulaketi akuimira. Ŵerengani ndime 1, ndi kumsonyeza mwininyumbayo mmene angapezere yankho. Mungampemphe kuti aŵerenge ndime 2. Ndiyeno nenani kuti: “Mogwirizana ndi nkhani imeneyi, kodi funso ili mungaliyankhe bwanji? [Ŵerenganinso funsolo, ndipo muloleni mwininyumbayo kuti ayankhe.] Mukuona kuti m’ndime iliyonse muli malemba. Malembawa amatithandiza kuona yankho la Baibulo pa mafunso amenewa. Mwachitsanzo, tiyeni tiŵerenge 2 Timoteo 3:16, 17 ndipo tione ngati likugwirizana ndi yankho limene munapereka ponena za mlembi wa Baibulo.” Mutaŵerenga ndime 3, kuyankha funso lake, ndi kuŵerenga Yohane 17:3, chititsani mwininyumba kulingalira za chidziŵitso chimene wapeza mwa kubwereza Phunziro 1. Tsopano mukhoza kupita ku Phunziro 2 ndi kuŵerenga funso lomalizira lakuti, “Kodi ndi njira ziŵiri ziti zimene tingaphunzirire za Mulungu?” Ndiyeno funsani kuti: “Kodi ndi liti pamene mungakhale ndi mphindi 15 kuti tikaphunzire Phunziro 2 ndi kupeza yankho lake?”
7 Ndi bwino kuti kukambirana kwanu kusakhale kovuta ndiponso nthaŵi zonse pamene kuli kotheka muyamikireni mwininyumbayo. Pamene mukupangana za kudzachezanso, m’malo momfunsa ngati akufuna kudzapitiriza, ingomulimbikitsani kutsatira njira yofananayo kaamba ka phunziro lotsatira. Iye adziŵe kuti inu mudzabweranso. Mungalimbikitsenso wophunzirayo kuti boloshalo alisunge pamalo abwino ndi oyenerera kuti asadzavutike kulipeza pamene mufikanso.
8 Khalani Otsimikiza: Pamene kuli kwakuti kuti tipambane chinsinsi chake ndi kukonzekera, tiyenera kukhala otsimikiza kuchita zinthu. Kuphunzitsa phunziro lonse m’mphindi zoŵerengeka ndi kovuta, choncho tsimikizirani kuyeserera ulalikiwo nthaŵi zochuluka ngati mmene kungafunikire kotero kuti musadodome posonyeza phunzirolo. Yesani kusonyeza phunziro kwa aliyense amene mungakumane naye panyumba ndi mwamwayi. Ngati zili kukuvutani kuyambitsa phunziro la Baibulo, musakhumudwe. Kuti tikhoze kuyambitsa maphunziro a Baibulo pamafunika kutsimikizira ndi kukhaladi ndi chikhumbo chouza ena choonadi.—Agal. 6:9.
9 Mwa kugwiritsa ntchito malingaliro amenewa, inunso mungakhale ndi mwayi wothandiza munthu wina kupeza njira yomuka kumoyo, mwa kuyambitsa ndi kuchititsa phunziro la Baibulo mu bolosha la Mulungu Amafunanji.—Mat. 7:14.