Sonyezani Kuti Mukulimbika pa ‘Kusala Mwazi’
1 Nthaŵi yafikanso yoti aliyense akonzenso khadi lake la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu limene timakhala nalo nthaŵi zonse kuti lititeteze ku kuikidwa magazi amene sitiwafuna. Ndi nthaŵinso yoti makolo amene ali ndi ana ang’onoang’ono akonzenso ma Identity Card a anawo kaamba ka chitetezo. Kukonzanso makadiwa ndi chinthu chabwino kwambiri potithandiza ife tonse ‘kusala mwazi.’—Mac. 15:29.
2 Koma kodi ndi kofunikadi kumakonza makadi amenewa chaka chilichonse? Inde, kulidi kofunika! Pamene madokotala ena ndi anthu ena ogwira ntchito m’chipatala aona khadi limene lili ndi deti lopitirira chaka chimodzi m’mbuyomu, nthaŵi zina amati akukayika ngati lidakagwirabe ntchito. Ena a iwo amati ndi zosadziŵika ngati zimene zili pa khadilo zidakali chikhumbo chanu kapena ayi. Kumbali ina, deti latsopano limasonyeza kuti khadilo likufotokoza malingaliro amene muli nawo tsopano.
3 Choncho tikukuyamikani inu nonse amene mokhulupirika komanso mwanzeru mwakhala mukudzaza makadi atsopano chaka chilichonse. Ambiri a inu simunaikidwe magazi amene simuwafuna chifukwa munali ndi khadi latsopano, losayinidwa ndi lochitiridwa umboni pamene munachita ngozi kapena pamene munapita kuchipatala pazifukwa zina za mwadzidzidzi.
4 Chifuno ndi Ntchito ya Khadi la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu: Khadi la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu linalinganizidwa kuti lizikuyankhulirani pamene, ngati mwachita ngozi, inuyo mukukanika kuyankhula. Limadziŵitsa ogwira ntchito zachipatala onse za zikhumbo zanu—mankhwala amene mungafune kulandira ndi amene simungawafune. Kumbukirani kuti ndi ufulu wanu kusankha choti chichitidwe pathupi lanu. Motero, deti, siginecha yanu ndi masiginechala a mboni zanu ndi zofunika kwambiri kuti khadilo likhaledi la lamulo.
5 Popeza kuti ndi zotero, simuyenera kusiya makadiwa kunyumba pamene mukupita kuntchito ngakhale pamene mukukagula zinthu. Muyenera kukhala ndi khadi lanu nthaŵi zonse ndi kuliika poonekera bwino pamene lingapezeke mosavuta. (Anthu ena ogwira ntchito zachipatala atiuza kuti ndi bwino kuika khadili pamodzi ndi layisensi yoyendetsera galimoto popeza kuti kaŵirikaŵiri ndi imene amayamba kuyang’ana pamene akufuna kudziŵa munthu amene wakomoka.) Popeza kuti sitingalote kapena kusankha nthaŵi imene tidzalifuna, chodziikira pangozi yosakhala ndi khadili ndi chiyani?
6 Chifuno ndi Ntchito ya Identity Card: Ogwira ntchito zachipatala ndiponso lamulo limati ana ang’ono sangathe kupanga zosankha zofunika kwambiri pankhani ya thanzi lawo ndi mankhwala amene angafune kulandira. Iwo angaonenso kuti mwana wamng’ono alibe zikhulupiriro zakezake zolimba zachipembedzo. Motero ngati ana anu ali ndi zaka zosakwanira pa zimene lamulo la m’dziko lanu limavomereza ndipo ngati ali osabatizidwa, kukakhala kwa nzeru kudziŵikitsa anawo ndi khadi limene limasonyeza dzina, adiresi ndi nambala ya foni ya inu makolo. Izi zimatheketsa kuti makolo mudziŵitsidwe pakabuka vuto lofunika kuchipatala pamene ana anu ali kwina, kusukulu kaya koseŵera. Ndiyeno inuyo mudzatha kufotokoza zikhumbo zanu ponena za mankhwala amene mukuvomereza ndiponso zidzakuthandizani kupita kuchipatala mwamsanga kuti mukaone kuti zimene zikuchitika ndi zimene inu mukufuna.
7 Chitani Mwamsanga!: Mwamsanga utatha msonkhano umene nkhani ino idzakambidwa, Mboni zonse zobatizidwa zidzalandira makadi atsopano a Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu, ndipo amene ali ndi ana ang’onoang’ono osabatizidwa adzalandira Identity Card ya mwana aliyense. Musakadzaze makadiwa tsiku lomwelo pambuyo pa msonkhano. Mukawadzazire kunyumba mosamalitsa koma OSAKAWASAYINA. Makadi onse adzasayinidwe, kuchitiridwa umboni, ndi kulembapo deti pambuyo pa Phunziro la Buku la Mpingo lotsatira, moyang’aniridwa ndi wochititsa phunziro la buku. Musanasayine tsimikizirani kuti makadiwo adzazidwa bwino lomwe. Amene adzasayina monga mboni ayenera kumuonadi mwiniwake wa khadilo akulisayinira. Mwa kukonza mawu a pakhadili kuti agwirizane ndi mikhalidwe ndi zikhulupiriro zawo, ofalitsa osabatizidwa angalembe malangizo awoawo oti azigwiritsa ntchito iwo ndi ana awo.
8 Ndi bwino kusayina khadi lanu anthu amene mukufuna kuti akuchitireni umboni akuona, ndiye kenaka mbonizo nazo ndi kusayina khadilo. Zikatero basi zatheka! Ndiyeno kwa chaka chonse n’kumachisamalira chinthu chofunika ndi chothandiza chimenechi. Ena amanyalanyaza kwa chaka chonse, akumati adzalembabe, koma amapezeka kuti atha chaka akunyamula khadi losamaliza kudzazidwa. Iwo kwakukulukulu amakhala osatetezedwa. N’kuchitiranji zoterozo? Ena adikira kudzakonza khadi lawo tsiku loti maŵa lake akuchitidwa opaleshoni! Zoonadi, tonsefe timakhala otanganidwa, ndipo ndi ochepa chabe amene amaganiza kuti angapite kuchipatala usiku uno kapena maŵa ali mumkhalidwe wovuta kwambiri, komabe chonde musanyalanyaze kuopsa kwa nkhaniyi.
9 Ochititsa phunziro la buku afufuze kuti atsimikizire kuti onse amene ali m’gulu lawo alandira chithandizo chimene akufuna podzaza makadi a Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu. Khadili liyenera kudzazidwa lonse bwino lomwe kuti likhale loteteza bwino kwambiri mwalamulo. Ngati mutati mwachita zonsezi koma mwadzidzidzi, mosayembekezereka mukutsutsidwa kwambiri, itanani akulu a kwanu mwamsanga ndipo iwo adziŵitse komiti yoyankhula ndi chipatala yapafupi kwambiri ndi kwanuko kuti idzakuthandizeni. M’njira zambiri mudzawafuna kuti akuchirikizeni mwachikondi.—Mat. 25:36.