Tizigwiritsa Ntchito Kabuku ka Uthenga Wabwino Pophunzitsa Anthu
1. Kodi kabuku ka Uthenga Wabwino kanalembedwa bwanji?
1 Utumiki wa Ufumu wa July chaka chino, unanena kuti kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu ndi kamodzi mwa zinthu zimene timagwiritsa ntchito kwambiri pophunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Malemba amene ali m’kabukuka sanawagwire mawu, n’cholinga choti munthu amene tikuphunzira naye kabukuka azimva malembawa kuchokera m’Baibulo. Mabuku athu ambiri amalembedwa moti munthu azitha kuwerenga yekha n’kumvetsa uthenga wake. Koma kabuku ka Uthenga wabwino anakalemba m’njira yoti tizikambirana ndi munthu amene akufuna kuphunzira choonadi kuti akamvetse. Choncho tikamagawira kabukuka, tiziyesetsa kusonyeza munthu mmene timaphunzirira, n’cholinga choti aone kuti kuphunzira mfundo za m’Baibulo n’kosangalatsa.—Mat. 13:44.
2. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji kabuku ka Uthenga Wabwino pa ulendo woyamba?
2 Pa Ulendo Woyamba: Munganene kuti: “Masiku ano anthu ambiri amada nkhawa akaganiza za m’tsogolo. Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzayamba kuyenda bwino? [Yembekezerani ayankhe.] M’Baibulo muli uthenga wabwino umene ungatipatse chiyembekezo. Taonani ena mwa mafunso amene mayankho ake amapezeka m’Baibulo.” M’patseni kabukuka n’kumupempha kuti asankhe funso pa mafunso amene ali kuseri kwa kabukuka. Kenako musonyezeni mmene timaphunzirira pogwiritsa ntchito ndime yoyamba pamutu umene wasankhawo. Njira ina ndi kufunsa mwininyumbayo funso lomwe lingamuchititse chidwi logwirizana ndi mutu umene inuyo mwasankha. Kenako mungapite naye pamutu umene pakupezeka funsolo, n’kumusonyeza mmene kabukuka kangamuthandizire kupeza yankho la funsolo. Ofalitsa ena amakonda kumuonetsanso vidiyo yogwirizana ndi mutuwo ngati ilipo pa webusaiti yathu ya jw.org/ny.
3. Fotokozani mmene tingagwiritsire ntchito kabukuka pochititsa phunziro.
3 Mmene Tingachititsire Phunziro Pogwiritsa Ntchito Kabukuka: (1) Werengani funso lomwe lili ndi nambala kuti muthandize mwininyumbayo kupeza mfundo yofunika. (2) Werengani ndime imene ili pansi pa funsolo. (3) Werengani lemba, kapena malemba omwe ali ndi mawu akuti, “werengani” ndipo kenako funsani mafunso othandiza mwininyumba kuona mmene lembalo likuyankhira funso lomwe lili ndi nambala lija. (4) Ngati pali ndime ina pansi pa funso lija, bwerezani mfundo 2 ndi 3. Ngati pali vidiyo yomwe ingathandize kuyankha funsolo, ndipo simunamuonetsepo mwininyumbayo, mungamuonetse pamene mukukambirana naye. (5) Funsani mwininyumbayo funso lija kuti muone ngati wamvetsa.
4. Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito kabuku kameneka mwaluso?
4 Yesetsani kukadziwa bwino kabukuka ndipo muzikagwiritsa ntchito mukakumana ndi munthu wachidwi. Musanayambe kuphunzira, ganizirani mmene zinthu zilili pa moyo wa munthuyo komanso fotokozani malemba omwe ali m’phunzirolo m’njira yomwe ingamuthandize kuwamvetsa bwino. (Miy. 15:28; Mac. 17:2, 3) Mukazolowera kugwiritsa ntchito kabukuka, mudzayamba kukakonda kwambiri pamene mukuphunzitsa anthu choonadi.