Ndandanda ya Mlungu wa October 5
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 5
Nyimbo Na. 109 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 19 ndime 18-23 ndi bokosi patsamba 198 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mbiri 1-4 (8 min.)
Na. 1: 1 Mbiri 1:28-42 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Tizikhala Okonzeka Kuuza Ena za Yehova—bt tsa. 140-141 ndime 4-5 (5 min.)
Na. 3: Kodi Wokana Khristu Ndi Ndani?—rs tsa. 414, Tanthauzo ndiponso ndime 1-2 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: ‘Muzichitira umboni mokwanira za uthenga wabwino.’—Mac. 20:24.
10 min: Zimene Munganene Pogawira Magazini a October. Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuchita zitsanzo ziwiri zosonyeza zimene tinganene pogawira magaziniwa pogwiritsa ntchito zitsanzo zaulaliki zomwe zili patsamba lino. Kenako kambiranani chitsanzo cha ulaliki chilichonse kuyambira poyambirira mpaka pamapeto.
10 min: Zofunika pampingo.
10 min: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anapindulira pogwiritsa ntchito malangizo a m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kulalikira M’gawo Lamalonda.” Kenako apempheni kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zomwe anakumana nazo.
Nyimbo Na. 98 ndi Pemphero