Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu September ndi October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! November ndi December: Buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena timapepala totsatirati: Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?, Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?, Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?, Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?, Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala?, Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka? ndi kakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
◼ Nkhani yapadera ya panyengo ya Chikumbutso cha 2016 idzakambidwa pa mlungu woyambira March 28. Mutu wa nkhaniyi tidzakudziwitsanibe. Mipingo imene idzakhale ndi mlungu wapadera kapena msonkhano wadera pa mlungu umenewu, idzakambe nkhaniyi mlungu wotsatira. Dziwani kuti nkhaniyi siyenera kukambidwa mlungu wa March 28 usanafike.