Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda October 1
“Tikugawira anthu m’dera lino magazini iyi. [Asonyezeni Nsanja ya Olonda ya October 1.] Anthu ena amaganiza kuti kupemphera n’kungotaya nthawi chifukwa palibe aliyense amene amamvetsera mapempherowo. Koma anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu amamvetsera mapemphero awo. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. [Werengani Yesaya 30:19.] M’magazini iyi muli mfundo zomwe zikusonyeza kuti Mulungu amamva ndiponso kuyankha mapemphero ngati munthu wapemphera moyenera komanso wapempha zinthu zoyenera.”
Galamukani! October
“Anthu ambiri amadabwa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika. Kodi mukuganiza kuti n’kupanda ulemu kufunsa Mulungu funso limeneli? [Yembekezerani ayankhe.] Nayenso Yobu, yemwe anali munthu wolungama, ankaona kuti atapeza mwayi wofunsa Mulungu, akanamufunsa mafunso omwe ankafuna kudziwa mayankho ake. [Werengani Yobu 23:3-5.] Magaziniyi ili ndi mayankho a m’Baibulo a mafunso atatu amene anthu ambiri, atapatsidwa mwayi, angakonde kumufunsa Mulungu.”