Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda September 1
“Nthawi zina anthu amachita zinthu zoipa chifukwa chotengeka ndi zinthu zonyenga zimene chipembedzo chawo chimaphunzitsa. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chimawachititsa kuti azinyengedwe kwambiri choncho? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena. [Werengani 1 Yohane 4:1.] Magazini iyi ikufotokoza kufunika koyerekezera zimene timakhulupirira ndi zimene Mawu a Mulungu amanena.” Kenako, muonetseni nkhani imene ikuyambira patsamba 10.
Galamukani! September
Werengani Mateyo 5:39. Kenako, funsani kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yesu ankatanthauza kuti tiyenera kungoyang’ana ena akamatichitira zoipa? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani yodziteteza ndiponso yokadandaula kukhoti.” Kenako muonetseni nkhani imene ikuyambira patsamba 10.
Nsanja ya Olonda October 1
“Anthu azipembedzo zosiyanasiyana amapemphera. Kodi mukuganiza kuti Mulungu amamvetseradi ndi kuyankha mapemphero? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limatilimbikitsa kupemphera. [Werengani Afilipi 4:6, 7.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa mafunso 7 okhudza pemphero amene anthu ambiri amafunsa.”
Galamukani! October
“Nthawi zambiri timamva za anthu amene amachitidwa zachinyengo ndi amuna kapena akazi awo, anthu andale, ndiponso anthu ena. Kodi mukuganiza kuti kupeza anthu oti mungawakhulupirire n’kovuta? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri amaona kuti lemba ili likukwaniritsidwa. [Werengani 2 Timoteyo 3:1-5.] Magazini iyi ikufotokoza kumene mungapezebe anthu okhulupirika.”