Zimene Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda July 1
“Anthu ambiri sadziwa zimene anganene kwa mnzawo amene akudwala kwambiri kapena amene ali ndi matenda osachiritsika. Kodi mukuganiza bwanji za malangizo awa? [Werengani Yakobe 1:19, ndipo yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ili ndi mfundo zingapo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 10.
Galamukani! July
“Kodi akazi ayenera kukhala atumiki mu mpingo? [Yembekezani ayankhe.] Tamvani zimene Baibulo limanena zokhudza mkazi wina. [Werengani Aroma 16:1.] Ngakhale zili choncho, vesi linanso limanena kuti akazi ayenera kukhala chete mu mpingo. Ndiyeno kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani kwenikweni pa nkhani imeneyi? Nkhani iyi ikufotokoza zimenezi.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 28.
Nsanja ya Olonda August 1
“Anthu ambiri amachita mantha kwambiri poganiza kuti nkhondo yanyukiliya kapena kusintha kwa nyengo kudzawononga dziko lathuli. Kodi mukuganiza kuti zimenezi zidzachitikadi? [Yembekezani ayankhe.] Onani zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. [Werengani Chivumbulutso 11:18.] Magazini iyi ikuyankha mafunso anayi amene anthu amakonda kufunsa pa nkhani yokhudza mapeto a dzikoli.”
Galamukani! August
“Mosakayikira, a Mboni za Yehova analankhulapo nanu. Kodi mumadabwa kuti n’chifukwa chiyani amayenda kunyumba ndi nyumba, ngakhale kuti anthu ambiri sasangalala ndi zimenezi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Mateyo 24:14.] Anthu ambiri sadziwa zoona zenizeni zokhudza ife? Magaziniyi ikufotokoza zambiri zokhudza Mboni za Yehova.”