Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda July 1
“Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kupeza mtendere wa mumtima m’dziko lamavutoli? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena pa Afilipi 4:6, 7. [Werengani.] Nkhani iyi ikufotokoza zimene tingachite kuti tikhale ndi mtendere umene Mulungu amapereka.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 10.
Galamukani! July
“Ambirife timayamikira kwambiri zimene makolo athu anatiphunzitsa. Koma kodi mukuganiza kuti kungakhale kupanda ulemu ngati mutaunika bwinobwino zimene munaphunzitsidwa muli mwana kuchipembedzo chimene munabadwira? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani 1 Yohane 4:1.] Nkhani iyi ikufotokoza ngati zili zoyenera kusintha chipembedzo chanu kapena ayi.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 28.
Nsanja ya Olonda August 1
“Ena amati zipembedzo zonse ndi njira zotsogolera kwa Mulungu mmodzi. Kodi inuyo mumaona kuti zipembedzo zonse n’zabwino? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Mateyo 7:13, 14.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo zitatu za m’Baibulo zimene chipembedzo chabwino chiyenera kulimbikitsa.”
Galamukani! August
“Tonsefe tinayamba tachitiridwapo tsankho. Kodi mukuganiza kuti Mulungu amawaona bwanji anthu a tsankho? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Machitidwe 10:34, 35.] Baibulo lingatithandize kupirira ena akamatisala. Lingatithandizenso kuti tithetse mtima wa tsankho umene tingakhale nawo. Magazini iyi ikufotokoza bwino nkhani imeneyi.”