Ndandanda ya Mlungu wa August 10
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 10
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 23, ndime 19-23 ndi bokosi, tsa. 239
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 7-9
Na. 1: Numeri 9:1-14
Na. 2: Kodi Ndi Mapwando Onse Amene Amakondweretsa Mulungu? (lr-CN mutu 29)
Na. 3: Njira Zimene Timasonyezera Kukhulupirika Kwathu kwa Yehova
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.10: Mabuku Ogawira mu August. Chitani chitsanzo chosonyeza njira imene yakhala yothandiza m’gawo lanu. Ndiponso, chitani chitsanzo chosonyeza zimene mungachite pogawira bukulo ndi cholinga choti muyambitse phunziro la Baibulo.
Mph.10: Ulongosoleni Ufumuwo. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 280, ndime 1, mpaka tsamba 281, ndime 2.
Mph.10: “Pulogalamu ya Tsiku la Msonkhano Wapadera wa 2010.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.