Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda August 1
“Anthu ambiri amakhulupirira kuti anthu onse abwino adzapita kumwamba. Kodi inunso mumakhulupirira zimenezi? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo likunena zokhudza dziko lapansi. [Werengani Salmo 37:11, 29.] Nkhani iyi ikufotokoza zimene Yesu anaphunzitsa zokhudza tsogolo la anthu pano padziko lapansi.” Asonyezeni nkhani imene ikuyambira patsamba 22.
Galamukani! August
“Imfa ya mayi kapena bambo imakhala yopweteka kwambiri. Kodi mukuvomereza zimenezi? [Yembekezerani ayankhe.] Ambiri amalimbikitsidwa ndi mavesi a m’Baibulo monga ili. [Werengani Chivumbulutso 21:4.] Nkhani iyi ikufotokoza zimene munthu angachite, makamaka wachinyamata, ngati ali ndi chisoni chachikulu chifukwa cha imfa ya mayi kapena bambo ake.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 10.
Nsanja ya Olonda September 1
“Anthu ena amanena kuti ngati uli wokhulupirika kwa Mulungu, iye adzakudalitsa ndi chuma koma ngati sakondwera nawe adzakupatsa umphawi. Kodi inuyo mumakhulupirira zotani pankhani imeneyi? [Yembekezerani ayankhe.] N’zochititsa chidwi kuti Yesu sanali wolemera. [Werengani Luka 9:58.] Magazini iyi ikufotokoza madalitso amene atumiki a Mulungu angayembekezere.”
Galamukani! September
“Kodi mukuganiza kuti achinyamata masiku ano akukumana ndi mavuto ambiri kusiyana ndi kale? [Yembekezerani ayankhe.] Anthu ambiri amaganiza kuti vesi ili limafotokoza bwino nthawi imene tiliyi. [Werengani 2 Timoteyo 3:1.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zingathandize makolo ndiponso achinyamata kupirira mavuto amenewa.”