Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda February 1
“Kodi mukuganiza kuti Mulungu amamva mapemphero onse? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Yesu ananena pankhani imeneyi. [Werengani Mateyo 6:7.] Nkhani yabwino iyi ikuyankha mafunso anayi amene anthu amakonda kufunsa kwambiri pankhani ya pemphero. Ndipo mayankho ake ndi ochokera m’Baibulo.” Kenako musonyezeni nkhani imene ikuyambira patsamba 16.
Galamukani! February
“Anthu ambiri amakhulupirira kuti zimene zimatichitikira pa moyo wathu zinalembedweratu. Kodi inunso mumakhulupirira zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Malinga ndi zimene vesi ili likunena, tili ndi ufulu wosankha. [Werengani Deuteronomo 30:19.] Nkhani iyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zosonyeza ngati zili zoona kuti Mulungu analemberatu zimene zimatichitikira pamoyo.” Kenaka musonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 12.
Nsanja ya Olonda March 1
“Kodi mukuganiza kuti zinthu zonse zimene zimachitika zinalembedweratu? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo likunena pankhaniyi. [Werengani Mlaliki 9:11.] Magazini iyi ikufotokoza kuti, ngakhale kuti Mulungu anakonzeratu zoti zinthu padziko lapansi zidzakhala bwino, amatipatsa ufulu wosankha zimene tikufuna kuchita pamoyo wathu.”
Galamukani! March
“Anthu ambiri masiku ano amadwala chifukwa choganizira kwambiri ndalama, makamaka masiku ovuta pankhani yazachuma ano. Kodi mukuvomereza kuti zimenezi zimachitika? [Yembekezani ayankhe.] Onani malangizo othandiza awa. [Werengani 1 Timoteyo 6:8, 10.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo zina za m’Baibulo zimene zingatithandize pankhani ya mmene tingagwiritsire ntchito ndalama zathu kuti tikhale ndi mtendere wa mu mtima.”