Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda April 1
“Mabuku ena amanena kuti Yesu sanafere ku Gologota monga mmene Baibulo limanenera koma amati anakwatira ndipo anabereka ana. Kodi munamvapo zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] M’pofunika kudziwa zoona pankhani imeneyi. [Werengani Yohane 17:3.] Nkhani iyi ikupereka zifukwa zake tiyenera kukhulupirira zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu.” Muonetseni nkhani imene yayambira patsamba 26.
Galamukani! April
Werengani Salmo 37:9-11. Ndiyeno funsani kuti: “Kodi mukuganiza kuti dziko lidzakhala bwanji malonjezo amenewa akadzakwaniritsidwa? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ikutchula ulosi wolimbikitsa kwambiri ndiponso ikufotokoza chifukwa chake masiku ano pali mavuto ambiri.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 20.
Nsanja ya Olonda May 1
“Kodi munayamba mwadzifunsapo chifukwa chake Mulungu amalola kuti tizivutika? [Yembekezani ayankhe.] Munthu wina amene analemba nawo Baibulo, anafunsa funso limene anthu ambiri amakonda kufunsa. [Werengani Salmo 10:1.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza chifukwa chake Mulungu walolera kuti anthu azivutika ndiponso zimene iye akuchita kuti athetse mavutowo.”
Galamukani! May
“Anthu ambiri amafuna atasiya kusuta koma amalephera. Kodi pali winawake amene mukumudziwa amene akufuna kusiya kusuta? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ena aona kuti n’zothandiza kupempha anzawo ndiponso abale awo kuti awathandize. [Werengani Mlaliki 4:12a.] Magazini iyi ikutchula mfundo zina zimene zingathandize munthu kuti asiye kusuta fodya.”