Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda March 1
“N’zovuta kwambiri kuti munthu uchite zabwino ngati anzako amakukakamiza kuchita zoipa. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chingatithandize kusagonja anzathu akamatikakamiza kuchita zoipa? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Miyambo 29:25.] Nkhaniyi ndi yothandiza ndipo ikufotokoza zifukwa zisanu zimene tiyenera kuopera Mulungu osati anthu.” Musonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 12.
Galamukani! March
“Tonsefe timafuna kukhala ndi mabwenzi abwino. Kodi mumafuna kuti mabwenzi anu akhale ndi makhalidwe otani? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo likunena. [Werengani Miyambo 17:17.] Nkhaniyi ili ndi mfundo zimene zingakuthandizeni kusankha mabwenzi abwino ndiponso kuti inuyo mukhale bwenzi labwino kwa anzanu.” Musonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 18.
Nsanja ya Olonda April 1
“Ndikufuna kumva maganizo anu pa mawu a Yesu awa. [Werengani Yohane 3:3.] Kodi mukuganiza kuti kubadwanso kumatanthauza chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Kumvetsa bwinobwino zimene Yesu ananena kungakhudze moyo wathu ndiponso tsogolo lathu. Magaziniyi ikufotokoza chifukwa chake ndikunena zimenezi.”
Galamukani! April
“Zikuoneka kuti ana a sukulu ambiri amakhala opanikizika. Kodi mukuganiza kuti zinthu zinali choncho ndi makolo awo pamene anali kusukulu? [Yembekezani ayankhe.] Kupanikizika kwambiri kumabweretsa mavuto aakulu. [Werengani Mlaliki 7:7a.] Magaziniyi ikufotokoza zimene zingathandize ana kulimbana ndi vutoli.”