Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda May 1
“Kodi mukuganiza kuti zinthu zikanakhala bwino padzikoli munthu aliyense akanati azitsatira mawu a Yesu awa?” [Werengani Mateyo 7:12. Kenako yembekezerani ayankhe.] Nkhani iyi ikufotokoza zinthu zina zimene Yesu anaphunzitsa zimene zikusonyeza zinthu zomwe Mkhristu weniweni ayenera kuchita.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 16.
Galamukani! May
“Kodi mukuganiza kuti mavuto a zachuma amene ali padzikoli atha posachedwapa? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri samadziwa mmene Baibulo lingatithandizire m’nthawi yovuta ino. [Werengani lemba limene lili m’nkhaniyi.] Nkhani iyi ikusonyeza mmene malangizo a m’Baibulo angatithandizire kupirira tikakumana ndi vuto la ndalama.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 18.
Nsanja ya Olonda June 1
“Masiku ano m’matchalitchi ambiri samalalikira za uchimo kusiyana ndi mmene zinkakhalira m’mbuyomu. Kodi mumakhulupirira kuti nkhani ya uchimo ndi yachikalekale, kapena mumaona kuti ndi nkhani yofunika kuiganizira kwambiri? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Aroma 5:12.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya uchimo.”
Galamukani! June
“Anthu ena akuona kuti zinthu zopanikiza zikuchulukirachulukirabe. Kodi mukuona kuti zimenezi ndi zoona? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri amaona kuti chifukwa chimodzi chimene chikuchititsa kuti tizikhala opanikizika kwambiri ndi ichi. [Werengani 2 Timoteyo 3:1.] Magazini iyi ikufotokoza mmene zinthu zopanikiza zimakhudzira moyo wathu. Ikufotokozanso mfundo zina zimene zingatithandize kuti tisamakhale opanikizika kwambiri.”