Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda November 1
“Zikuoneka kuti mabanja ambiri akukumana ndi zinthu zosautsa kwambiri. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chingachitikire mabanja ngati am’banjamo atamatsatira maganizo a Yesu awa? [Werengani Mateyo 20:28. Kenako dikirani ayankhe.] Nkhani iyi ikufotokoza zinthu zisanu zimene mabanja angaphunzire kwa Yesu.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 16.
Galamukani! November
“Kodi mukuona kuti zipembedzo zimalimbikitsa kuti anthu azikondana ndiponso kukhala mwamtendere kapena kuti anthu azidana ndi kuchitirana chiwawa? [Yembekezerani ayankhe.] Zikuoneka kuti ambiri satsatira mawu a Yesu awa. [Werengani Mateyo 5:44, 45.] Nkhani iyi ikuyankha funso lakuti, Kodi n’zotheka munthu kukonda adani ake?” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 10.
Nsanja ya Olonda December 1
“Kodi mukuganiza kuti tsiku lina Mulungu angadzathetse mavuto padzikoli? [Yembekezerani ayankhe.] Lonjezo la m’Baibulo ili likutipatsa chifukwa choyembekezera zabwino. [Werengani lemba limodzi pa malemba amene ali m’bokosi patsamba 7.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza nthawi ndiponso mmene Mulungu adzathetsere mavuto onse.”
Galamukani! December
“Ena amakhulupirira kuti zinthu za padzikoli ndi za kumwambaku zinachita kulengedwa, pamene enanso amati zinangokhalako zokha ndipo zilibe cholinga chenicheni. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena. [Werengani Aheberi 3:4.] Magaziniyi ikufotokoza bwino kumene kunachokera zinthuzi ndiponso cholinga chake.”