Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda November 1
“Kodi mumaganiza kuti angelo amachita chidwi ndi zochita zathu? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limanena mfundo yochititsa chidwi iyi. [Werengani Luka 15:10.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Yesu ananena zokhudza zolengedwa zauzimu komanso mmene zochita zawo zimatikhudzira.” Kenako, muonetseni nkhani imene ikuyambira patsamba 16.
Galamukani! November
Werengani 2 Timoteyo 3:16. Kenako funsani kuti: “Kodi inuyo mumaona kuti tiyenera kukhulupirira chilichonse chimene Baibulo limanena? [Yembekezani ayankhe.] Zimene nkhani iyi ikufotokoza zikusonyeza kuti zimene mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi ndi mabuku a mbiri yakale amanena zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena zokhudza dziko lakale la Iguputo.” Kenako, muonetseni nkhani imene ikuyambira patsamba 15.
Nsanja ya Olonda December 1
“Anthu ambiri amakhulupirira kuti kumalo amizimu kuli mizimu imene imalamulira zochita zathu. Kodi inu mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Chivumbulutso 12:7-9.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza amene amakhala ku malo amizimu, mmene zochita zawo zimatikhudzira komanso ngati zili zotheka kulankhulana nawo.”
Galamukani! December
“Kodi munayamba mwaganizapo kuti ndi chifukwa chiyani anthu amakondwerera Khirisimasi pa 25 December ngakhale kuti Baibulo silinena tsiku limene Yesu anabadwa? [Yembekezani ayankhe.] Zomwe vesi ili likufotokoza zikusonyeza kuti sizingatheke kuti Yesu anabadwa m’nyengo imeneyi yomwe imakhala nyengo yozizira kumadera a kumpoto kwa dziko lapansili. [Werengani Luka 2:8.] Magazini iyi ikufotokoza chiyambi cha miyambo ina yotchuka imene imachitika nthawi ya Khirisimasi.”