Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Pa July 23-25, 2010, tinali ndi msonkhano wachigawo ku Civo Stadium ndipo msonkhanowu unalumikizidwa pa telefoni ndi msonkhano umene unachitikira ku Kamuzu Stadium ku Blantyre ndi ku Mzuzu Stadium ku Mzuzu. Pa msonkhanowu m’bale Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la m’Chichewa. Chiwerengero cha anthu amene anapezeka pa misonkhano yonse itatuyi chinali 56,295 ndipo panabatizidwa anthu 487.