Zilengezo
◼ November: Gawirani kabuku kakuti Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani? December: Gawirani buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati pakhomopo pali ana mungagawire buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. January 2011: Gawirani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ndipo mu February gawirani buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
◼ Kuyambira mlungu wa January 10, 2011, tidzayamba kuphunzira buku lakuti ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’ pa Phunziro la Baibulo la Mpingo. Musaitanitse mabukuwa chifukwa tidzatumizira mpingo uliwonse potengera chiwerengero cha ofalitsa ndipo tidzaphatikizapo ena owonjezera.