Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda June 1
“Anthu ambiri amakhulupirira kuti zipembedzo za m’dzikoli ndi njira zosiyanasiyana zopita kwa Mulungu mmodzi. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Onani zimene Baibulo limanena. [Werengani Yoswa 24:15.] Nkhaniyi ikufotokoza zifukwa zomveka zimene ifeyo patokha tiyenera kuona ngati chipembedzo chathu chimalambiradi Mulungu woona.” Asonyezeni nkhani imene ikuyambira patsamba 12.
Galamukani! June
“Tonsefe timadziwa anthu ena amene anamwalira. Kodi mukuganiza kuti tiyenera kuopa kuti ena mwa iwo angatikwiyire n’kutivulaza? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Mlaliki 9:5, 6.] Nkhaniyi ndi yolimbikitsa kwambiri.” Asonyezeni nkhani imene ikuyambira patsamba 22.
Nsanja ya Olonda July 1
“Anthu ambiri amene ali ndi Baibulo amaona kuti n’lovuta kulimvetsa. Kodi inuyo mumaonanso choncho? [Yembekezani ayankhe.] Malinga ndi vesili, Mlembi Wamkulu wa Baibulo amafuna kuti tiwamvetse bwino ndiponso tipindule nawo Mawu ake. [Werengani Salmo 119:130.] Magazini ino ikupereka mfundo zitatu zimene zingatithandize kuti tilimvetse bwino Baibulo.”
Galamukani! July
“Anthu ambiri masiku ano akudwala matenda ovutika maganizo. Kodi mukuganiza kuti Mulungu amasamalira anthu amenewa aliyense payekha? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Salmo 34:18.] Magazini ino ikufotokoza mmene Mulungu angathandizire anthu amene akuvutika maganizo, ngakhale kuti angafunikirenso thandizo la kuchipatala. Ikufotokozanso zimene tinganene polimbikitsa anthu amenewa.”