Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda January 1
“Kodi mukuganiza kuti Mulungu zimamukhudza anthu akamawononga zachilengedwe? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Chivumbulutso 11:18.] Nkhani iyi ikufotokoza zimene Malemba amanena zomwe zimatipatsa chiyembekezo kuti dzikoli lidzakonzedwanso.” Asonyezeni nkhani imene ili patsamba 18.
Galamukani! January
“Anthu ambiri akakumana ndi mavuto, amaganiza kuti Mulungu akuwalanga. Kodi inunso munaganizapo choncho? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Yakobe 1:13.] Nkhani iyi ikufotokoza zimene zimachititsa mavuto athu. Ikufotokozanso zifukwa zokhulupirira kuti mavuto adzatha posachedwapa.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 28.
Nsanja ya Olonda February 1
“Kodi mumaganiza kuti Mulungu amavomereza zipembedzo zonse? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Yesu ananena palemba ili. [Werengani Mateyo 15:8, 9.] Nkhani iyi ikufotokoza mfundo zotithandiza kudziwa ngati Mulungu amavomereza zipembedzo zonse.” Asonyezeni nkhani imene ili patsamba 9.
Galamukani! February
“Mmene dzikoli lilili, limasonyeza kuti linapangidwa kuti pakhale zamoyo. Kodi mukuganiza kuti zimenezi zinangochitika zokha, kapena zimasonyeza kuti kuli Mlengi? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri amavomereza zimene Baibulo limanena palemba ili. [Werengani Salmo 104:24.] Magazini iyi ikufotokoza umboni wa sayansi ndiponso wa m’Malemba wakuti kuli Mlengi.”