Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/10 tsamba 4
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 1/10 tsamba 4

Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Nsanja ya Olonda January 1

“Kodi mukuganiza kuti zinthu zikanakhala bwino padzikoli aliyense akanati azitsatira mfundo iyi? [Werengani Aroma 12:18. Dikirani kuti ayankhe.] Ndiyeno kodi munayamba mwadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani m’mbuyomo Mulungu analamula anthu ake kuti akamenyane ndi mitundu ina ya anthu? Nkhani iyi ikuyankha funso limeneli m’njira yomveka bwino, malingana ndi zimene Baibulo limanena.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 13.

Galamukani! January

Werengani Machitidwe 17:31a. Ndiyeno nenani kuti: “Anthu ambiri akamva za Tsiku la Chiweruzo amachita mantha kwambiri. Kodi inunso mumaliopa tsikuli? [Dikirani kuti ayankhe.] Baibulo limatiuza kuti Tsiku la Chiweruzo lidzabweretsa madalitso ambiri padziko lapansi. Nkhani iyi ikufotokoza zimenezi.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 10.

Nsanja ya Olonda February 1

“Anthu ambiri amakhulupirira kuti adzapita kumwamba akadzamwalira. Kodi inunso zimakusangalatsani zokakhala kumwamba? [Dikirani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena zokhudza mphotho imene Mulungu adzapereke kwa anthu ambiri. [Werengani Salmo 37:29.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pankhani ya amene adzapite kumwamba ndiponso zimene azikachita kumeneko.”

Galamukani! February

“Masiku ano anthu ambiri amasudzulana. Kodi mukuganiza kuti ambiri mwa anthu amenewa amaganizira bwino zonse zofunikira kuziganizira asanafike posudzulana? [Dikirani ayankhe. Ndiyeno werengani Miyambo 14:15.] Magazini ino ikufotokoza zinthu zinayi zimene anthu amene akuganiza zosudzulana ayenera kuziona bwinobwino.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena