Ndandanda ya Mlungu wa February 8
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 8
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 3 ndime 8-15, ndi bokosi la patsamba 30a
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Oweruza 11–14
Na. 1: Oweruza 13:1-14
Na. 2: Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Mawu a Yesu Opezeka pa Luka 16:9-13?
Na. 3: Kodi Mawu a M’buku la Chivumbulutso Akuti ‘Kuzunzidwa kwa Muyaya’ Amatanthauza Chiyani? (rs tsa. 147 ndime 3 ndi 4)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kuyankha Mafunso Okhudza Maholide. Kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Kukambitsirana, kuyambira patsamba 241 ndime 4 mpaka tsamba 243 ndime 2. Kodi anthu a m’dera lanu amakonda kuchita zikondwerero ziti? Kodi ndi malo ati kumene mungalalikire panthawi ya chikondwerero chinachake? Chitani chitsanzo chosonyeza kholo likuthandiza mwana wake mmene angayankhire ngati atafunsidwa kuti, ‘N’chifukwa chiyani sukondwerera Isitala?’
Mph. 20: “Kugawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Musanakambirane ndime 2, gawirani aliyense kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso, ngati muli nato, ndipo fotokozani mbali zosiyanasiyana za kapepalako. Mukamaliza kukambirana ndime 2, wofalitsa achite chitsanzo chosonyeza mmene angagawirire kapepalaka. Funsani woyang’anira utumiki kapena mkulu wina kuti afotokoze zimene mpingo wakonza panthawi yogawira timapepalati.
a [Mawu a M’munsi]
Mungasankhe kukambirana bokosi kapena ayi.