Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda September 1
“Anthu ambiri amaganiza kuti nkhani ya Adamu ndi Hava ya m’buku la Genesis ndi yongopeka. Koma ena amakhulupirira kuti Adamu ndi Hava anali anthu enieni. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Yesu ananena. [Werengani Maliko 10:6-9.] Nkhaniyi ikuunika umboni wokhudza nkhani imeneyi ndipo ikusonyeza kuti zimene timakhulupirira pankhaniyi n’zofunika kwambiri.” Sonyezani nkhani imene yayambira patsamba 12.
Galamukani! September
Werengani 1 Yohane 4:8. Ndiyeno nenani kuti: “Anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu amalanga ndi moto anthu oipa. Ena amaona kuti maganizo amenewa sagwirizana ndi zimene tawerengazi. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Nkhaniyi ikufotokoza zimene Baibulo limaphunzitsa.” Sonyezani nkhani yomwe yayambira patsamba 10.
Nsanja ya Olonda October 1
“Tonsefe timakumana ndi mavuto. [Tchulani ena mwa mavuto amene anthu amakumana nawo m’gawo lanu.] Kodi mukuganiza kuti Mulungu angatithandize kuthetsa mavuto amenewa? [Yembekezani ayankhe.] Pavesi ili Yesu anatchula njira imodzi imene Mulungu amatithandizira. [Werengani Luka 11:13.] Magaziniyi ikuthandizani kudziwa kuti mzimu woyera n’chiyani komanso kudziwa mmene ungakuthandizireni.”
Galamukani! October
“Banja lililonse limakumana ndi mavuto. Kodi mukuganiza kuti mabanja angapeze kuti malangizo odalirika? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Salmo 32:8.] Galamukani! iyi ndi yapadera ndipo ikufotokoza mfundo zingapo za m’Baibulo zimene zingathandize kwambiri mabanja.”