Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Ndife osangalala kukudziwitsani kuti kuwonjezera pa mzinda wa Blantyre ndi wa Lilongwe, tsopano tayambanso kugwiritsa ntchito dongosolo lapadera lolalikira m’malo opezeka anthu ambiri mumzinda wa Mzuzu. Munthu wina ataona zimenezi anayamikira ndipo ananena kuti: “Tsopano sindizivutikanso kupeza mabuku anu. Ndizingobwera pano kudzatenga.” Njira imeneyi ikuthandiza kuti tizilalikira kwa anthu ambiri ndipo ikuyenda bwino m’mizinda yonse ya Blantyre, Lilongwe ndi Mzuzu. Posachedwapa tiyambanso kugwira ntchitoyi mumzinda wa Zomba.