Ndandanda ya Mlungu wa October 12
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 12
Nyimbo Na. 9 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 20 ndime 1-7 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mbiri 5-7 (8 min.)
Na. 1: 1 Mbiri 6:48-60 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Kodi Mpatuko N’chiyani?—rs tsa. 299 ndime 1-tsa. 301 ndime 2 (5 min.)
Na. 3: Mnzako Weniweni Amanena Zoona—lv bokosi tsa. 167 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Khalani “ozikika mozama” ndiponso ‘okhazikika m’chikhulupiriro.’—Akol. 2:6, 7.
10 min: Khalani “Ozikika Mozama” Ndiponso ‘Okhazikika M’chikhulupiriro.’ Nkhani yochokera pa mutu wa mwezi uno. Kodi kukhala “ozikika mozama” ndiponso ‘okhazikika m’chikhulupiriro’ kumatanthauza chiyani? Nanga tingachite bwanji zimenezi? (Onani Nsanja ya Olonda ya June 1, 1998, tsamba 10-12.) Werengani lemba la Akolose 2:6, 7; Aheberi 6:1 ndi Yuda 20, 21 ndipo fotokozani mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’malemba amenewa pa moyo wathu. Pomaliza tchulani nkhani zimene tiphunzire mu Msonkhano wa Utumiki mwezi uno, ndipo kambiranani kugwirizana kwake ndi mutu wa mwezi uno.
20 min: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muziphunzitsa Anthu Amene Mumaphunzira Nawo Baibulo Kuti Azikonda Kuphunzira Paokha.” Nkhani yokambirana. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa waluso akuthandiza munthu amene amaphunzira naye Baibulo mmene angafufuzire yankho la funso pogwiritsa ntchito Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani.
Nyimbo Na. 116 ndi Pemphero