Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa October
“Tikukambirana mwachidule ndi anthu a m’dera lino nkhani yokhudza ulamuliro wabwino. Kodi mukuganiza kuti pali boma limene lingathetse mavuto monga chiwawa komanso kupanda chilungamo padzikoli?” Yembekezerani ayankhe. Kenako kumbutsani munthuyo zoti m’pemphero lachitsanzo, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. Ufumuwu ndi umene udzathetse mavuto padzikoli. Ndiyeno musonyezeni nkhani yomwe ili patsamba lomaliza m’magazini ya Nsanja ya Olonda ya October 1, ndipo kambiranani mfundo zomwe zili pa funso loyamba. Muwerenge lemba limodzi mwa malemba amene ali pamenepo. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zodzabweranso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda October 1
“Tikucheza mwachidule ndi anthu m’dera lino ndipo tikukambirana nawo mawu awa, a m’pemphero lomwe ambiri amalidziwa bwino. Yesu ndi amene anauza otsatira ake kuti azinena zimenezi popemphera. [Werengani Mateyu 6:9, 10.] Kodi munthu atakufunsani mungathe kumufotokozera bwinobwino kuti Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Nanga mukudziwa chifukwa chake Yesu ankakonda kutchula za Ufumuwu akamaphunzitsa anthu? [Yembekezerani ayankhe.] Magaziniyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza Ufumu wa Mulungu. Ikufotokozanso zinthu zabwino zimene Ufumuwu udzachitire anthu padzikoli.”
Galamukani! October
“Tikukambirana mwachidule ndi anthu ndipo tikuwasonyeza mmene angapezere yankho la funso ili. [Awonetseni funso limene lili pachikuto cha magaziniyo.] Kodi mukuganiza kuti chuma n’chimene chimasonyeza kuti munthu zikumuyendera bwino? [Yembekezerani ayankhe.] M’Baibulo muli mfundo zomwe zingatithandize kuti tiziona nkhani imeneyi moyenera. [Werengani Luka 12:15.] Baibulo limasonyeza kuti munthu aliyense zinthu zikhoza kumamuyendera bwino. Magaziniyi ikufotokoza zimene tingachite kuti zinthu zizitiyendera bwino.”