Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa October
“Masiku ovuta ano, tonsefe tikukumana ndi mavuto amene akudetsa nkhawa mabanja. Kodi mukuganiza kuti tingapeze kuti malangizo odalirika amene angatithandize kuti tikhale ndi mabanja osangalala?” Yembekezani ayankhe. Kenako m’patseni mwininyumbayo Nsanja ya Olonda ya October 1, ndiyeno kambiranani nkhani imodzi pansi pa timitu timene tili patsamba 16 ndi 17 ndiponso lemba limodzi. Gawirani magaziniwo ndipo mukonze zoti mudzabwerereko kudzakambirana funso limodzi pa mafunso otsalawo.
Nsanja ya Olonda October 1
Sonyezani chithunzi chimene chili pachikuto cha magaziniyi, ndiyeno funsani kuti, “Kodi mungamve bwanji ngati mutazindikira kuti munthu wina anakunamizani zinazake zokhudza Mulungu? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Yesu ananena zimene zingatithandize kusiyanitsa zoona ndi zabodza. [Werengani Yohane 17:17.] Pamenepatu ndi Baibulo lokha limene limatiuza zoona zenizeni zokhudza Mulungu. Magazini iyi ili ndi mayankho a m’Baibulo a nkhani zimene anthu amanena zonamizira Mulungu.”
Galamukani! October
“Lero tikugwira ntchito imene cholinga chake ndi kuthandiza mabanja. Kodi mukuganiza kuti vuto lalikulu limene makolo akukumana nalo polera ana ndi vuto liti? [Yembekezani ayankhe.] Makolo ambiri amapeza malangizo m’Baibulo. Mwachitsanzo, mawu anzeru otsatirawa ndi othandiza polangiza ana. [Werengani Aefeso 4:31.] Magazini iyi ikufotokoza mmene malangizo a m’Baibulo angathandizire makolo kulera bwino ana awo, kuyambira ali akhanda mpaka kukula.”