Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa October
“Lero tikucheza ndi athu osiyanasiyana koma mwachidule. Ambiri amene tacheza nawo anena kuti pa mavuto onse amene akumana nawo, imfa ya munthu amene amamukonda imakhala yopweteka kwambiri. Kodi inuyo mumaonanso choncho? [Yembekezani ayankhe.] Komabe pali nkhani ina yolimbikitsa kwambiri.” Musonyezeni nkhani yomwe ili patsamba lomaliza m’magazini ya Nsanja ya Olonda ya October 1, ndipo kambiranani mfundo zomwe zili pa funso loyamba. Muwerenge lemba limodzi mwa malemba amene ali pamenepo. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zodzabweranso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda October 1
“Tikulimbikitsa anzathu kuti aziwerenga Baibulo. Tikudziwa kuti anthu ena amakonda kuwerenga Baibulo koma ena sakonda kuliwerenga. Kodi inuyo mumakonda kuliwerenga? [Yembekezani ayankhe.] Koma taonani kuti Baibulo limanena mosapita m’mbali amene ali mwiniwake. [Werengani 1 Atesalonika 2:13.] Choncho ngati Baibulo ndi buku lochokera kwa Mulungu, kodi sindiye kuti m’pofunika kumaliwerenga? Magaziniyi ikufotokoza mwachidule kuti Baibulo ndi buku lotani komanso chifukwa chake tiyenera kulikonda.”
Galamukani! October
“Tikufuna kumva maganizo anu pa funso ili: Kodi n’zotheka kukhala okhutira ngakhale tilibe chuma? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi. [Werengani 1 Timoteyo 6:8.] Magaziniyi ikufotokoza mmene tiyenera kuonera chuma komanso ikunena zinthu zitatu zofunika kwambiri zomwe sitingathe kugula ndi ndalama.”