Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Bambo wina atakumana ndi Mboni za Yehova ku Kawale mumzinda wa Lilongwe, anakhulupirira kuti Mboni za Yehova zimaphunzitsa choonadi. Ngakhale kuti anali ndi udindo ku mpingo wawo anayamba kupezeka pamisonkhano yathu. Tsiku loyamba limene anapezeka pamisonkhano yathu sanavale taye koma ulendo wotsatira anavala. Kholo lake limodzi silinalole kuti aziphunzira ndi Mboni koma bamboyu sanasiye kuphunzira ndipo anapita patsogolo mwauzimu. Tsopano anabatizidwa pamodzi ndi mkazi wake. Ana ake aakazi awiri nawonso akuphunzira Baibulo. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Ngati tingathandize mwamuna kuphunzira Baibulo, nthawi zambiri banja lake lonse limaphunziranso. Tiyenitu tipitirize kuthandiza amuna a mtundu uliwonse.—1 Tim. 2:4.