Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa May
“Tikucheza mwachidule ndi anthu ndipo tikukambirana nawo funso ili. [Asonyezeni funso lomwe lili patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya May 1.] Kodi inuyo mukuganiza kuti ndi ndani akulamulira dzikoli?” Yembekezani ayankhe. Kambiranani ndime zimene zili pansi pa funso loyamba komanso lemba limodzi pa malemba amene ali kumapeto kwa ndimezo. Agawireni magaziniyo, ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda May 1
“Tikukambirana ndi anthu mwachidule chifukwa anthu ambiri amafuna atadziwa za tsogolo lawo. Kodi inuyo mukaganizira za m’tsogolo mumaona kuti zinthu zidzakhala bwanji? [Yembekezerani ayankhe. Kenako werengani lemba limodzi pa malemba omwe ali m’bokosi lakuti, “Zomwe Mulungu Waneneratu Zokhudza Zimene Zidzachitike M’tsogolo.”] Magaziniyi ikufotokoza zinthu zina zimene Mulungu ananeneratu kuti zidzachitika m’tsogolo. Ikufotokozanso chifukwa chake tingakhulupirire kuti zimenezi zidzachitikadi.”
Galamukani! May
“Tabwera kuti tikambirane nanu mwachidule mfundo zimene zingathandize anthu amene akuvutika maganizo ndi zinazake. Kodi mukuona kuti masiku ano anthu ambiri akuvutika maganizo kusiyana ndi kale? [Yembekezani ayankhe.] Malangizo amene ali m’Baibulo athandizapo anthu ambiri kuthana ndi vuto limeneli. Mwachitsanzo, taonani malangizo awa. [Werengani Mateyu 6:34.] Magaziniyi ikufotokoza mmene mfundo za m’Baibulo zingatithandizire kuthana ndi kuvutika maganizo komwe nthawi zambiri kumayamba chifukwa cha zinthu 4.”
Dziwani izi: Magazini imeneyi ingathandize kwambiri abizinezi.