Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa February
“Anthu ambiri ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya Baibulo. Ena amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu, pamene ena amaliona kuti ndi lofanana ndi mabuku ena onse. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?” Yembekezerani ayankhe. Ndiyeno musonyezeni nkhani yomwe ili patsamba lomaliza m’magazini ya Nsanja ya Olonda ya February 1, ndipo kambiranani mfundo zomwe zili pa funso loyamba. Muwerenge lemba limodzi mwa malemba amene ali pamenepo. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zodzabweranso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda February 1
“Anthu ambiri amafuna kuti padziko lonse lapansi pasamachitike nkhondo. Kodi inuyo mukuganiza kuti nkhondo zingathe, padziko lonse n’kukhala mtendere? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani zimene lemba ili likunena. [Werengani Salimo 46:9.] N’zochititsa chidwi kuti zinthu zimene zinachitika pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse komanso pambuyo pake, ndi umboni woti Yehova akwaniritsa lonjezo limeneli posachedwapa, ndipo padzikoli sipadzakhalanso nkhondo. Magaziniyi ikufotokoza mmene zimenezi zidzachitikire.”
Galamukani! February
“Tikukambirana ndi anthu mwachidule za vuto limene limakhudza anthu ambiri. Zikuoneka kuti anthufe sitikhala ndi nthawi yokwanira kuchita zonse zofunika. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chimachititsa kuti nthawi zonse tizikhala otanganidwa? Kodi n’chifukwa choti timakhala ndi zochita zambiri, kapena n’chifukwa choti timawononga nthawi pa zinthu zosafunika? [Yembekezerani ayankhe.] Anthu ambiri sadziwa kuti m’Baibulo muli malangizo amene angatithandize kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi. Mwachitsanzo, taonani lemba ili. [Werengani Afilipi 1:10a.] Magaziniyi ikufotokoza njira 4 zimene zathandiza anthu ambiri kuti azigwiritsa ntchito bwino nthawi yawo.”