Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda February 1
“Kodi mumaona kuti n’zothekadi kudziwa kuti kodi Mulungu ndi wotani? [Yembekezani ayankhe.] Ndili ndi mfundo yochititsa chidwi pa nkhani imeneyi.” Werengani ndi kukambirana mfundo zimene zili pansi pa funso 2 patsamba 16 komanso limodzi mwa malemba amene ali m’nkhaniyo. Gawirani magaziniwo, ndipo gwirizanani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane mfundo za pa funso 3.
Galamukani! February
“Chifukwa chakuti Baibulo ndi buku lakale kwambiri, anthu ena amaona ngati kuti silinganene zolondola pa nkhani yasayansi. Kodi inuyo maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri amadabwa akaona kuti Baibulo limanena zimene zili pa lemba ili. [Werengani Yesaya 40:22.] Nkhani imene yayambira patsamba 22 ikuyankha funso lakuti, Kodi Sayansi ndi Baibulo Zimagwirizana?”
Nsanja ya Olonda March 1
“Mboni za Yehova zimadziwika chifukwa cha ntchito yolalikira imene zimagwira. Kodi munayamba mwadabwapo chifukwa chimene timachitira ntchito imeneyi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mawu awa. [Werengani Mateyu 24:14.] Magazini iyi ikuyankha mafunso awa: Kodi uthenga wabwino umene atchulawu ndi chiyani? Kodi Ufumu wa Mulungu ndi chiyani? Kodi mapeto amene adzafikewo ndi chiyani?”
Galamukani! March
“Popeza kuti anthu ambiri akuvutika ndi matenda, tikugawana ndi anthu mfundo yolimbikitsa imene ili pa vesi ili. [Werengani Yesaya 33:24.] Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzasintha motani lemba limeneli likadzakwaniritsidwa? [Yembekezani ayankhe.] Pamene tikuyembekezera kuti Mulungu adzasinthe zinthu ngati mmene vesili likunenera, pali mfundo zofunika zimene tonse tingatsatire kuti thanzi lathu lizikhala labwinopo. Mfundo zimenezi zafotokozedwa m’magazini iyi.”